Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 10:4 - Buku Lopatulika

4 Aukometsa ndi siliva ndi golide; auchirikiza ndi misomali ndi nyundo, kuti usasunthike.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Aukometsa ndi siliva ndi golide; auchirikiza ndi misomali ndi nyundo, kuti usasunthike.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Anthu ena amakongoletsa chosemacho ndi siliva ndi golide, kenaka nkuchikhomerera ndi misomali, kuti chisagwedezeke.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Amakongoletsa chosemacho ndi siliva ndi golide; kenaka amachikhomerera ndi misomali kuti chisagwedezeke.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 10:4
9 Mawu Ofanana  

Mafano ao ndiwo a siliva ndi golide, ntchito za manja a anthu.


Mafano a amitundu ndiwo siliva ndi golide, ntchito ya manja a anthu.


Wachipala achita zake ndi nsompho, nagwira ntchito ndi makala, nafanizira fanolo ndi nyundo, nagwira ntchito yake ndi mkono wake wamphamvu; inde, ali ndi njala, ndipo mphamvu zake zilephera; iye samwa madzi, nalefuka.


Amene ataya golide, namtulutsa m'thumba, ndi kuyesa siliva ndi muyeso, iwo alemba wosula golide; iye napanga nazo mulungu; iwo agwada pansi, inde alambira.


Iwo amanyamula mlunguwu paphewa, nausenza, naukhazika m'malo mwake, nukhala chilili; pamalo pakepo sudzasunthika; inde, wina adzaufuulira, koma sungathe kuyankha, kapena kumpulumutsa m'zovuta zake.


Ndipo tsopano aonjeza kuchimwa, nadzipangira mafano oyenga a siliva wao, mafano monga mwa nzeru zao, onsewo ntchito ya amisiri; anena za iwo, Anthu ophera nsembe apsompsone anaang'ombe.


Tsoka iye wakunena kwa mtengo, Galamuka; ndi kwa mwala wosalankhula, Nyamuka! Kodi ichi chiphunzitsa? Taona chakutidwa ndi golide ndi siliva, ndi m'kati mwake mulibe mpweya konse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa