Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 1:3 - Buku Lopatulika

3 Anamdzeranso masiku a Yehoyakimu mwana wake wa Yosiya, mfumu ya Yuda, kufikira Zedekiya mwana wake wa Yosiya mfumu ya Yuda atatsiriza zaka khumi ndi chimodzi; kufikira a ku Yerusalemu anatengedwa ndende mwezi wachisanu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Anamdzeranso masiku a Yehoyakimu mwana wake wa Yosiya, mfumu ya Yuda, kufikira Zedekiya mwana wake wa Yosiya mfumu ya Yuda atatsiriza zaka khumi ndi chimodzi; kufikira a ku Yerusalemu anatengedwa ndende mwezi wachisanu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Chauta adalankhula nayenso pa nthaŵi ya Yehoyakimu, mwana wa Yosiya mfumu ya ku Yuda, mpaka mwezi wachisanu wa chaka cha khumi ndi chimodzi cha Zedekiya, mwana wa Yosiya mfumu ya ku Yuda, pamene anthu a ku Yerusalemu adatengedwa ukapolo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Yehova anayankhulanso naye pa nthawi yonse ya ulamuliro wa Yehoyakimu mwana wa Yosiya mfumu ya Yuda, mpaka mwezi wachisanu wa chaka cha 11 cha ufumu wa Zedekiya mwana wa Yosiya mfumu ya Yuda, pamene anthu a ku Yerusalemu anapita ku ukapolo.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 1:3
19 Mawu Ofanana  

Ndipo Farao Neko analonga ufumu Eliyakimu mwana wa Yosiya, m'malo mwa Yosiya atate wake, nasanduliza dzina lake likhale Yehoyakimu; koma anapita naye Yehowahazi, nafika iye mu Ejipito, nafa komweko.


Ndipo mfumu ya Babiloni analonga Mataniya mbale wa atate wake akhale mfumu m'malo mwake, nasanduliza dzina lake likhale Zedekiya.


Ndi ana a Yosiya: woyamba Yohanani, wachiwiri Yehoyakimu, wachitatu Zedekiya, wachinai Salumu.


Ndipo anadza kwa ine mau a Yehova, kuti,


Mau amene anadza kwa Yeremiya kuchokera kwa Yehova, pamene Nebukadinezara mfumu ya Babiloni, ndi nkhondo yake yonse, ndi maufumu onse a dziko lapansi amene anagwira mwendo wake, ndi anthu onse, anamenyana ndi Yerusalemu, ndi mizinda yake yonse, akuti,


Mau amene anadza kwa Yeremiya kuchokera kwa Yehova masiku a Yehoyakimu mwana wa Yosiya, mfumu ya Yuda, kuti,


Tenga buku lampukutu, nulembe m'menemo mau onse ndanena kwa iwe akunenera Israele, ndi akunenera Yuda, ndi akunenera amitundu onse kuyambira tsiku ndinanena kwa iwe, kuyambira masiku a Yosiya, mpaka lero.


Chaka chakhumi ndi chimodzi cha Zedekiya, mwezi wachinai, tsiku lachisanu ndi chinai, mzinda unabooledwa.


Nena kwa anthu onse a m'dziko, ndi kwa ansembe, kuti, Muja mukasala ndi kulira mwezi wachisanu, ndi wachisanu ndi chitatu, zaka izi makumi asanu ndi awiri, kodi mukasalira Ine, Inedi?


Atero Yehova wa makamu: Kusala kwa mwezi wachinai, ndi kusala kwa mwezi wachisanu, ndi kusala kwa mwezi wachisanu ndi chiwiri, ndi kusala kwa mwezi wakhumi kukhale kwa nyumba ya Yuda chimwemwe ndi chikondwerero, ndi nyengo zoikika zosekerera; chifukwa chake kondani choonadi ndi mtendere.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa