Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 1:1 - Buku Lopatulika

1 Mau a Yeremiya mwana wa Hilikiya, wa ansembe amene anali ku Anatoti m'dziko la Benjamini;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Mau a Yeremiya mwana wa Hilikiya, wa ansembe amene anali ku Anatoti m'dziko la Benjamini;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Aŵa ndi mau a Yeremiya, mwana wa Hilikiya, mmodzi mwa ansembe a ku Anatoti, m'dziko la Benjamini.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Mawu a Yeremiya mwana wa Hilikiya, mmodzi mwa ansembe a ku Anatoti, mʼdziko la Benjamini.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 1:1
23 Mawu Ofanana  

Ndipo mfumu inanena ndi Abiyatara wansembeyo, Pita ku Anatoti ku minda yako; pakuti wakutidwa ndi imfa; koma sindikupha iwe lero lino, chifukwa unanyamula likasa la Ambuye Yehova pamaso pa Davide atate wanga, ndi popeza unanzunzidwa monse umo atate wanga Davide anazunzidwamo.


ndi ku fuko la Benjamini Geba ndi mabusa ake, ndi Alemeti ndi mabusa ake, ndi Anatoti ndi mabusa ake. Mizinda yao yonse mwa mabanja ao ndiyo mizinda khumi ndi itatu.


Ndipo Yeremiya anamlembera Yosiya nyimbo yomlira; ndi oimbira onse, amuna ndi akazi, amanena za Yosiya nyimbo za maliro zao mpaka lero lino; naziika zikhale lemba mu Israele; taonani, zilembedwa mu Nyimbo za Maliro.


nachita choipa pamaso pa Yehova Mulungu wake; sanadzichepetse kwa Yeremiya mneneri wakunena zochokera pakamwa pa Yehova.


kuti akwaniridwe mau a Yehova pakamwa pa Yeremiya, mpaka dziko linakondwera nao masabata ake; masiku onse a kupasuka kwake linasunga Sabata, kukwaniritsa zaka makumi asanu ndi awiri.


Chaka choyamba tsono cha Kirusi mfumu ya ku Persiya, kuti akwaniridwe mau a Yehova m'kamwa mwa Yeremiya, Yehova anautsa mzimu wa Kirusi, kuti abukitse mau mu ufumu wake wonse, nawalembenso, ndi kuti,


Anthu a ku Anatoti, zana limodzi mphambu makumi awiri kudza asanu ndi atatu.


Masomphenya a Yesaya mwana wa Amozi, amene iye anaona, onena za Yuda ndi Yerusalemu, masiku a Uziya, Yotamu, Ahazi, ndi Hezekiya, mafumu a Yuda.


Fuula ndi mau ako iwe mwana wamkazi wa Galimu! Tamva, iwe Laisa! Iwe Anatoti wosauka!


Mau amene Yesaya mwana wa Amozi anaona, onena za Yuda ndi Yerusalemu.


Chifukwa chake atero Yehova za anthu a Anatoti, amene afuna moyo wanga, kuti, Usanenere m'dzina la Yehova, ungafe ndi mkono wathu;


Ndipo tsopano, walekeranji kumdzudzula Yeremiya wa ku Anatoti, amene amadziyesa mneneri wanu,


Mau amene anadza kwa Yeremiya kuchokera kwa Yehova, kuti,


pamenepo Yeremiya anatuluka mu Yerusalemu kumuka kudziko la Benjamini, kukalandira gawo lake kumeneko.


anadzadi mau a Yehova kwa Ezekiele wansembe, mwana wa Buzi, m'dziko la Ababiloni kumtsinje Kebara; ndi pomwepo dzanja la Yehova lidamkhalira.


chaka choyamba cha ufumu wake, ine Daniele ndinazindikira mwa mabuku kuti chiwerengo chake cha zaka, chimene mau a Yehova anadzera nacho kwa Yeremiya mneneri, kunena za makwaniridwe a mapasuko a Yerusalemu, ndizo zaka makumi asanu ndi awiri.


Mau a Amosi, amene anali mwa oweta ng'ombe a ku Tekowa, ndiwo amene anawaona za Israele masiku a Uziya mfumu ya Yuda, ndi masiku a Yerobowamu mwana wa Yowasi mfumu ya Israele, zitatsala zaka ziwiri chisanafike chivomezi.


Pamenepo Amaziya wansembe wa ku Betele anatumiza kwa Yerobowamu mfumu ya Israele, ndi kuti, Amosi wapangira inu chiwembu pakati pa nyumba ya Israele; dziko silingathe kulola mau ake onse.


Ndipo iwo anati, Ena ati, Yohane Mbatizi; koma ena, Eliya; ndipo enanso Yeremiya, kapena mmodzi wa aneneri.


Pomwepo chinachitidwa chonenedwa ndi Yeremiya mneneri, kuti,


Pamenepo chinakwaniridwa chonenedwa ndi Yeremiya mneneri, ndi kuti, Ndipo iwo anatenga ndalamazo zasiliva makumi atatu, mtengo wa uja wowerengedwa mtengo wake, amene iwo a ana a Israele anawerenga mtengo wake;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa