Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Rute 4:6 - Buku Lopatulika

6 Ndipo woombolera anati, Sindikhoza kuuombola kwa ine ndekha, ndingaononge cholowa changa; udzitengere wekha mphamvu yanga yakuombola; popeza sinditha kuombola.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Ndipo woombolera anati, Sindikhoza kuuombola kwa ine ndekha, ndingaononge cholowa changa; udzitengere wekha mphamvu yanga yakuombola; popeza sinditha kuombola.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Apo wachibaleyo adati, “Sindingathe kugula mundawo kuti ukhale wanga, kuwopa kuti ndingaononge choloŵa changa. Mugule ndinu, ine sindingathe.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Pamenepo wachibaleyo anati, “Sindingathe kuwuwombola mundawu kuti ukhale wanga, kuopa kuti kutaya cholowa changa. Mugule ndinu. Ine sindingathe.”

Onani mutuwo Koperani




Rute 4:6
8 Mawu Ofanana  

Ndipo Yuda anati kwa Onani, Lowani naye mkazi wa mbale wako, ndi kumchitira mkazi zoyenera mphwake wa mwamuna wake, ndi kumuukitsira mkulu wako mbeu.


Mbale wako akasaukira chuma, nakagulitsa chakechake, pamenepo mombolo wake, mbale wake weniweni azidza, naombole chimene mbale wake anagulitsacho.


Ndipo ngati mwamunayo safuna kutenga mkazi wa mbale wake, mkazi wa mbale wakeyo azikwera kunka kuchipata, kwa akulu, ndi kuti, Mbale wa mwamuna wanga akana kuutsira mbale wake dzina mu Israele; safuna kundichitira ine zoyenera mbale wa mwamuna.


Pamenepo akulu a mzinda wake amuitane, ndi kulankhula naye; ndipo akaimirira ndi kuti, Sindifuna kumtenga;


pamenepo mkazi wa mbale wake azimyandikiza pamaso pa akulu, nachotse nsapato yake ku phazi la mwamunayo, ndi kumthira malovu pankhope pake, ndi kumyankha ndi kuti, Atere naye mwamuna wosamanga nyumba ya mbale wake.


Nati Naomi kwa mpongozi wake, Yehova amdalitse amene sanaleke kuwachitira zokoma amoyo ndi akufa. Ndipo Naomi ananena naye, Munthuyo ndiye mbale wathu, ndiye mmodzi wa iwo otiombolera cholowa.


Gona usiku uno, ndipo kudzali m'mawa, akakuombolera, chabwino, akuombolere; koma ngati safuna kukuombolera, pali Yehova, ndidzakuombolera cholowa ndine; gona mpaka m'mawa.


Nati iye, Ndiwe yani? Nayankha iye, Ndine Rute mdzakazi wanu; mufunde mdzakazi wanu chofunda chanu, pakuti inu ndinu wondiombolera cholowa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa