Rute 4:4 - Buku Lopatulika4 ndipo ndati ndikuululira ichi, ndi kuti, Ugule aka pamaso pa nzika, ndi pamaso pa akulu a anthu a kwathu. Ukafuna kuombola ombola; koma ukapanda kuombola, undiuze, ndidziwe; pakuti palibe woombola koma iwe, ndi ine pambuyo pako. Pamenepo anati, Ndidzaombola. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20144 ndipo ndati ndikuululira ichi, ndi kuti, Ugule aka pamaso pa nzika, ndi pamaso akulu a anthu a kwathu. Ukafuna kuombola ombola; koma ukapanda kuombola, undiuze, ndidziwe; pakuti palibe woombola koma iwe, ndi ine pambuyo pako. Pamenepo anati, Ndidzaombola. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa4 Choncho ndinaganiza zokuuza zimenezi, kuti ugule mundawo pamaso pa anthu amene ali panoŵa, ndi pamaso pa atsogoleri a abale athu. Ngati ufuna kugula, ugule. Koma ngati sufuna, undiwuze kuti ndidziŵe, pakuti palibe wina woti augule koma iweyo, ndipo pambuyo pa iwe pali ine.” Munthuyo adati, “Ndigula munda umenewo.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero4 Choncho ndinaganiza zokuwuza zimenezi kuti ugule mundawu pamaso pa anthu amene ali panowa, ndi pamaso pa akuluakulu mwa abale athu. Ngati ukufuna kuwuwombola, uwombole. Koma ngati sukufuna, undiwuze kuti ndidziwe, pakuti palibe wina angawuwombole koma iweyo, ndipo pambuyo pa iwe pali ine.” Iye anati, “Ine ndidzawuwombola.” Onani mutuwo |