Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Rute 1:5 - Buku Lopatulika

5 Koma Maloni ndi Kilioni anamwalira onse awiri; motero ana ake aamuna awiri ndi mwamuna wake anamsiya mkaziyo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Koma Maloni ndi Kilioni anamwalira onse awiri; motero ana ake amuna awiri ndi mwamuna wake anamsiya mkaziyo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Koma Maloni ndi Kiliyoni adamwalira, kotero kuti Naomi adataya ana ake aŵiri aja, pamodzi ndi mwamuna wake yemwe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Maloni ndi Kiliyoni anamwaliranso kotero kuti Naomi anatsala yekha wopanda ana ake awiri aja ndi mwamuna wake.

Onani mutuwo Koperani




Rute 1:5
9 Mawu Ofanana  

Pamenepo udzati m'mtima mwako, Ndani wandibalitsa ine amenewa, popeza ana anga anachotsedwa kwa ine, ndipo ndili wouma, ndi wochotsedwa m'dziko, ndi woyendayenda kwina ndi kwina? Ndipo ndani wadza ndi awa? Taona ndinasiyidwa ndekha, amenewa anali kuti?


Choipa chako chidzakulanga iwe, mabwerero ako adzakudzudzula iwe; dziwa, nuone, kuti ichi ndi choipa ndi chowawa, kuti wasiya Yehova Mulungu wako, ndi kuti kundiopa Ine sikuli mwa iwe, ati Ambuye, Yehova wa makamu.


Ndipo pamene anayandikira kuchipata cha mzindawo, onani, anthu analikunyamula munthu wakufa, mwana wamwamuna mmodzi yekha, amake ndiye mkazi wamasiye; ndipo anthu ambiri amumzinda anali pamodzi naye.


Tapenyani tsopano kuti Ine ndine Iye, ndipo palibe mulungu koma Ine; ndipha Ine, ndikhalitsanso ndi moyo, ndikantha, ndichizanso Ine; ndipo palibe wakulanditsa m'dzanja langa.


Dzina la munthuyo ndiye Elimeleki, ndi dzina la mkazi wake ndiye Naomi, ndi maina a ana ake awiri ndiwo Maloni, ndi Kilioni; ndiwo Aefurati a ku Betelehemu ku Yuda. Iwowa ndipo analowa m'dziko la Mowabu, nakhala komweko.


Nadzitengera iwo akazi a ku Mowabu; wina dzina lake ndiye Oripa, mnzake dzina lake ndiye Rute; ndipo anagonera komweko ngati zaka khumi.


Pamenepo ananyamuka iyeyu ndi apongozi ake kuti abwerere kuchoka m'dziko la Mowabu; pakuti adamva m'dziko la Mowabu kuti Yehova adasamalira anthu ake ndi kuwapatsa chakudya.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa