Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 31:9 - Buku Lopatulika

9 Ndipo ana a Israele anagwira akazi a Amidiyani, ndi ana aang'ono, nafunkha ng'ombe zao zonse, ndi zoweta zao zonse, ndi chuma chao chonse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Ndipo ana a Israele anagwira akazi a Amidiyani, ndi ana ang'ono, nafunkha ng'ombe zao zonse, ndi zoweta zao zonse, ndi chuma chao chonse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Ndipo adagwira akazi a ku Midiyani ukapolo, pamodzi ndi ana ao. Adalandanso ng'ombe zao, nkhosa zao, ndi chuma chao chonse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Aisraeli anagwira ukapolo amayi a Chimidiyani ndi ana awo ndipo analandanso ngʼombe, ziweto zawo zina zonse ndi katundu wawo yense.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 31:9
9 Mawu Ofanana  

ndi chuma chao chonse ndi ana ao ndi akazi ao anawagwira, nafunkha zonse za m'nyumba.


Anakanthanso a m'mahema a ng'ombe, nalanda nkhosa zochuluka, ndi ngamira; nabwerera kunka ku Yerusalemu.


Chifukwa chake Yehova Mulungu wake anampereka m'dzanja la mfumu ya Aramu; ndipo anamkantha, natenga ndende unyinji waukulu wa anthu ake, nafika nao ku Damasiko. Anaperekedwanso iye m'dzanja la mfumu ya Israele, amene anamkantha makanthidwe aakulu.


Ndipo anatentha ndi moto mizinda yao yonse yokhalamo iwo, ndi zigono zao zonse.


Popeza wankhondo yense anadzifunkhira yekha.


Ndipo anapha mafumu a Amidiyani pamodzi ndi ophedwa ao ena; ndiwo Evi, ndi Rekemu, ndi Zuri, ndi Huri, ndi Reba, mafumu asanu a Amidiyani; namupha Balamu mwana wa Beori ndi lupanga.


Koma akazi ndi ana ndi ng'ombe ndi zonse zili m'mzindamo, zankhondo zake zonse, mudzifunkhire nokha; ndipo mudye zankhondo za adani anu, zimene Yehova Mulungu wanu anakupatsani.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa