Nehemiya 1:3 - Buku Lopatulika3 Nanena nane iwo, Otsalawo otsala andende uko kudzikoko akulukutika kwakukulu, nanyozedwa; ndi linga la Yerusalemu lapasuka, ndi zipata zake zatenthedwa ndi moto. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20143 Nanena nane iwo, Otsalawo otsala andende uko kudzikoko akulukutika kwakukulu, nanyozedwa; ndi linga la Yerusalemu lapasuka, ndi zipata zake zatenthedwa ndi moto. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa3 Adandiyankha kuti, “Anthu amene aja ali pa mavuto ndiponso ali ndi manyazi aakulu. Makoma a Yerusalemu ngogamukagamuka, ndipo zipata zake zidaonongeka ndi moto.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero3 Anandiyankha kuti, “Amene sanatengedwe ukapolo aja ali pa mavuto aakulu ndipo ali ndi manyazi. Khoma la Yerusalemu ndilogamukagamuka ndipo zipata zake zinatenthedwa ndi moto.” Onani mutuwo |
Pakuti atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Monga mkwiyo wanga ndi ukali wanga wathiridwa kwa okhala mu Yerusalemu, momwemo ukali wanga udzathiridwa pa inu, pamene mudzalowa mu Ejipito; ndipo mudzakhala chitukwano, ndi chizizwitso, ndi chitemberero, ndi chitonzo; ndipo simudzaonananso malo ano.