Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 8:28 - Buku Lopatulika

28 Ndipo pofika Iye kutsidya lina, kudziko la Agadara, anakomana naye awiri ogwidwa ndi ziwanda, akutuluka kumanda, aukali ndithu, kotero kuti sangathe kupitapo munthu panjira imeneyo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

28 Ndipo pofika Iye kutsidya lina, kudziko la Agadara, anakomana naye awiri ogwidwa ndi ziwanda, akutuluka kumanda, aukali ndithu, kotero kuti sangathe kupitapo munthu pa njira imeneyo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

28 Yesu atafika ku tsidya la nyanja, ku dera la Agadara, anthu aŵiri ogwidwa ndi mizimu yoipa adadzakumana naye kuchokera ku manda. Anali aukali kwambiri, kotero kuti panalibe munthu ndi mmodzi yemwe wotha kudzera njira imeneyo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

28 Ndipo atafika ku mbali ina ya dera la Gadara, anakumana ndi anthu awiri ogwidwa ndi ziwanda akuchokera ku manda. Iwowa anali woopsa kwambiri kotero kuti panalibe munthu akanatha kudzera njira imeneyo.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 8:28
9 Mawu Ofanana  

ndi Ayebusi, ndi Aamori, ndi Agirigasi;


ndi Aamori, ndi Akanani, ndi Agirigasi, ndi Ayebusi.


Ndipo mbiri yake inabuka ku Siriya konse: ndipo anatengera kwa Iye onse akudwala, ogwidwa ndi nthenda ndi mazunzo a mitundumitundu, ndi ogwidwa ndi ziwanda, ndi akhunyu, ndi amanjenje; ndipo Iye anawachiritsa.


Ndipo anazizwa anthuwo nanena, Ndiye munthu wotani uyu, pakuti ngakhale mphepo ndi nyanja zimvera Iye?


za Yesu wa ku Nazarete, kuti Mulungu anamdzoza Iye ndi Mzimu Woyera ndi mphamvu; amene anapitapita nachita zabwino, nachiritsa onse osautsidwa ndi mdierekezi, pakuti Mulungu anali pamodzi ndi Iye.


Pamene Yehova Mulungu wanu atakulowetsani m'dziko limene munkako kulilandira likhale lanulanu, ndipo atakataya amitundu ambiri pamaso panu, Ahiti, ndi Agirigasi, ndi Aamori, ndi Akanani, ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi, mitundu isanu ndi iwiri yaikulu ndi yamphamvu yoposa inu;


Masiku a Samigara, mwana wa Anati, masiku a Yaele maulendo adalekeka ndi apanjira anayenda mopazapaza.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa