Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 8:15 - Buku Lopatulika

15 Ndipo anamkhudza dzanja lake, ndipo malungo anamleka mkaziyo; ndipo anauka, namtumikira Iye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 Ndipo anamkhudza dzanja lake, ndipo malungo anamleka mkaziyo; ndipo anauka, namtumikira Iye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 Adakhudza amaiwo pa dzanja, ndipo malungowo adatha. Pomwepo amai aja adadzuka nayamba kukonzera Yesu chakudya.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 Ndipo Yesu anakhudza dzanja lake ndipo pomwepo anachira nayamba kumutumikira.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 8:15
15 Mawu Ofanana  

Ndipo anthu, pakuika maliro a munthu wina, anaona gulu la nkhondo, naponya mtembo m'manda mwa Elisa; koma pamene mtembowo unakhudza mafupa a Elisa, wakufayo anauka, naima chilili.


nakhudza nalo kukamwa kwanga nati, Taona ichi chakhudza milomo yako; ndipo mphulupulu zako zachotsedwa, zochimwa zako zaomboledwa.


ndipo anampempha Iye, kuti akhudze mphonje yokha ya chovala chake; ndipo onse amene anamkhudza anachiritsidwa.


Ndipo Yesu anagwidwa ndi chifundo, nakhudza maso ao; ndipo pomwepo anapenyanso, namtsata Iye.


Ndipo pofika Yesu kunyumba ya Petro, anaona mpongozi wake ali gone, alikudwala malungo.


Ndipo pakudza madzulo, anabwera nao kwa Iye anthu ambiri ogwidwa ndi ziwanda; ndipo Iye anatulutsa mizimuyo ndi mau, nachiritsa akudwala onse;


Ndipo Yesu anatambalitsa dzanja lake, namkhudza iye, nati, Ndifuna; takonzedwa. Ndipo pomwepo khate lake linachoka.


Ndipo onani, mkazi, anali ndi nthenda yachidwalire zaka khumi ndi ziwiri, anadza pambuyo pake, nakhudza mphonje ya chofunda chake;


Pomwepo anakhudza maso ao, nati, Chichitidwe kwa inu monga chikhulupiriro chanu.


Ndipo pomwepo, potuluka m'sunagoge, iwo analowa m'nyumba ya Simoni ndi Andrea pamodzi ndi Yakobo ndi Yohane.


Ndipo Yesu anagwidwa chifundo, natansa dzanja namkhudza iye, nanena naye, Ndifuna; khala wokonzedwa.


Ndipo Iye anamgwira dzanja lake, naitana, nati, Buthu, tauka.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa