Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 27:41 - Buku Lopatulika

41 Chomwechonso ansembe aakulu, pamodzi ndi alembi ndi akulu anamchitira chipongwe, nati,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

41 Chomwechonso ansembe aakulu, pamodzi ndi alembi ndi akulu anamchitira chipongwe, nati,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

41 Nawonso akulu a ansembe pamodzi ndi aphunzitsi a Malamulo ndi akulu a Ayuda ankamuseka. Ankati,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

41 Chimodzimodzinso akulu a ansembe, aphunzitsi amalamulo ndi akuluakulu anamuchitira chipongwe.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 27:41
12 Mawu Ofanana  

Nchokoma kodi kuti Iye akusanthuleni? Kodi mudzamnyenga Iye monga munyenga munthu?


Achite manyazi, nadodome iwo akukondwera chifukwa cha choipa chidandigwera. Avekeke ndi manyazi ndi kupunzika iwo akudzikuza pa ine.


Tsono musakhale amnyozo, kuti nsinga zanu zingalimbe; pakuti Ambuye, Yehova wa makamu, wandimvetsa za chionongeko chotsimikizidwa padziko lonse lapansi.


Atero Yehova, Mombolo wa Israele, ndi Woyera wake, kwa Iye amene anthu amnyoza, kwa Iye amene mtundu wathu unyasidwa naye, kwa mtumiki wa olamulira: Mafumu adzaona, nadzauka; akalonga nadzalambira chifukwa cha Yehova, amene ali wokhulupirika, ngakhale Woyera wa Israele, amene anakusankha Iwe.


Ndipo ndinatha abusa atatuwo mwezi umodzi; pakuti mtima wanga unalema nao, ndi mtima waonso unaipidwa nane.


nati, Nanga Iwe, wopasula Kachisi, ndi kummanganso masiku atatu, tadzipulumutsa wekha; ngati uli Mwana wa Mulungu, tatsika pamtandapo.


Anapulumutsa ena, sangathe kudzipulumutsa yekha. Ndiye mfumu ya Aisraele; atsike tsopano pamtandapo, ndipo tidzamkhulupirira Iye.


Pakuti adzampereka kwa amitundu, nadzamseka, nadzamchitira chipongwe, nadzamthira malovu;


Ndipo Yesu anati kwa ansembe aakulu ndi akapitao a Kachisi, ndi akulu, amene anadza kumgwira Iye, Munatuluka ndi malupanga ndi mikunkhu kodi monga ngati kugwira wachifwamba?


Ndipo anthu anaima alikupenya. Ndi akulunso anamlalatira Iye, nanena, Anapulumutsa ena; adzipulumutse yekha ngati iye ndiye Khristu wa Mulungu, wosankhidwa wake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa