Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 26:24 - Buku Lopatulika

24 Mwana wa Munthu achokatu, monga kunalembedwa za Iye; koma tsoka ali nalo munthu amene Mwana wa Munthu aperekedwa ndi iye! Kukadakhala bwino kwa munthuyo ngati sakadabadwa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

24 Mwana wa Munthu achokatu, monga kunalembedwa za Iye; koma tsoka ali nalo munthu amene Mwana wa Munthu aperekedwa ndi iye! Kukadakhala bwino kwa munthuyo ngati sakadabadwa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

24 Mwana wa Munthu akukaphedwadi, monga momwe Malembo akunenera za Iye. Komabe ali ndi tsoka munthu amene akukapereka Mwana wa Munthuyo. Kukadakhala bwino koposa kwa munthu ameneyo, akadapanda kubadwa.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

24 Mwana wa Munthu adzaphedwa monga mmene kunalembedwera za Iye. Koma tsoka kwa munthu amene apereka Mwana wa Munthu! Kukanakhala bwino kwa iye akanapanda kubadwa.”

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 26:24
34 Mawu Ofanana  

ndipo ndidzaika udani pakati pa iwe ndi mkaziyo, ndi pakati pa mbeu yako ndi mbeu yake; ndipo idzalalira mutu wako, ndipo iwe udzalalira chitendeni chake.


Imfa iwagwere modzidzimutsa, atsikire kumanda ali amoyo, pakuti m'mokhala mwao muli zoipa pakati pao.


Koma Inu, Mulungu, mudzawatsitsira kudzenje la chionongeko. Anthu okhetsa mwazi ndi achinyengo masiku ao sadzafikira nusu; koma ine ndidzakhulupirira Inu.


Ndipo atapita masabata makumi asanu ndi limodzi mphambu awiri wodzozedwayo adzalikhidwa, nadzakhala wopanda kanthu; ndi anthu a kalonga wakudzayo adzaononga mzinda ndi malo opatulika; ndi kutsiriza kwake kudzakhala kwa chigumula, ndi kufikira chimaliziro kudzakhala nkhondo; chipasuko chalembedweratu.


Ndipo ndidzatsanulira pa nyumba ya Davide, ndi pa okhala mu Yerusalemu, mzimu wa chisomo ndi wakupembedza; ndipo adzandipenyera Ine amene anandipyoza; nadzamlira ngati munthu alira mwana wake mmodzi yekha, nadzammvera zowawa mtima, monga munthu amvera zowawa mtima mwana wake woyamba.


Galamuka, lupanga, pa mbusa wanga, ndi pa munthu mnzanga wa pamtima, ati Yehova wa makamu; kantha mbusa, ndi nkhosa zidzabalalika; koma ndidzabwezera dzanja langa pa zazing'onozo.


Tsoka lili ndi dziko lapansi chifukwa cha zokhumudwitsa! Pakuti sikutheka kuti zokhumudwitsa zileke kudza, koma tsoka lili ndi munthu amene chokhumudwitsacho chidza ndi iye.


Pamenepo Yesu ananena kwa iwo, Inu nonse mudzakhumudwa chifukwa cha Ine usiku uno; pakuti kwalembedwa, Ndidzakantha mbusa, ndipo zidzabalalika nkhosa za gulu.


Koma pakutero malembo adzakwaniridwa bwanji, pakuti kuyenera chomwecho?


Koma izi zonse zinachitidwa, kuti zolembedwa za aneneri zikwaniridwe. Pomwepo ophunzira onse anamsiya Iye, nathawa.


Pakuti Mwana wa Munthu amukadi, monga kwalembedwa za Iye; koma tsoka munthuyo amene apereka Mwana wa Munthu! Kukadakhala bwino kwa munthu ameneyo ngati sakadabadwa iye.


Ndipo Iye ananena nao, Eliya ayamba kudza ndithu, nadzakonza zinthu zonse; ndipo kwalembedwa bwanji za Mwana wa Munthu, kuti ayenera kumva zowawa zambiri ndi kuyesedwa chabe?


Pakuti Mwana wa Munthu amukatu, monga kunaikidwiratu; koma tsoka munthuyo amene ampereka!


ndipo anati kwa iwo, Kotero kwalembedwa, kuti Khristu amve zowawa, nauke kwa akufa tsiku lachitatu;


Pamene ndinakhala nao, Ine ndinalikuwasunga iwo m'dzina lanu amene mwandipatsa Ine; ndipo ndinawasunga, ndipo sanatayike mmodzi yense wa iwo, koma mwana wa chitayiko, kuti lembo likwaniridwe.


Chifukwa chake anati wina kwa mnzake, Tisang'ambe awa, koma tichite maere, awa akhale a yani; kuti lembo likwaniridwe limene linena, Anagawana zovala zanga mwa iwo okha, ndi pa malaya anga anachitira maere. Ndipo asilikali anachita izi.


Chitapita ichi Yesu, podziwa kuti zonse zidatha pomwepo kuti lembo likwaniridwe, ananena, Ndimva ludzu.


ameneyo, woperekedwa ndi uphungu woikidwa ndi kudziwiratu kwa Mulungu, inu mwampachika ndi kumupha ndi manja a anthu osaweruzika;


Ndipo pamene adampangira tsiku, anadza kunyumba yake anthu ambiri; amenewo anawafotokozera, ndi kuchitira umboni Ufumu wa Mulungu, ndi kuwakopa za Yesu, zochokera m'chilamulo cha Mose ndi mwa aneneri, kuyambira mamawa kufikira madzulo.


kuti achite zilizonse dzanja lanu ndi uphungu wanu zidaweruziratu zichitike.


Pakuti ndinapereka kwa inu poyamba, chimenenso ndinalandira, kuti Khristu anafera zoipa zathu, monga mwa malembo;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa