Mateyu 21:42 - Buku Lopatulika42 Yesu ananena kwa iwo, Kodi simunawerenge konse m'malembo, Mwala umene anaukana omanga nyumba womwewu unakhala mutu wa pangodya: Ichi chinachokera kwa Ambuye, ndipo chili chozizwitsa m'maso mwathu? Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201442 Yesu ananena kwa iwo, Kodi simunawerenga konse m'malembo, Mwala umene anaukana omanga nyumba womwewu unakhala mutu wa pangodya: Ichi chinachokera kwa Ambuye, ndipo chili chozizwitsa m'maso mwathu? Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa42 Yesu adaŵafunsa kuti, “Kodi monga simudaŵerenge Malembo aja akuti, “ ‘Mwala umene amisiri omanga nyumba adaaukana, womwewo wasanduka mwala wapangodya, wofunika koposa. Ambuye ndiwo adachita zimenezi, ndipo nzotidabwitsa kwambiri.’ Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero42 Yesu anawawuza kuti, “Kodi simunawerenge mʼmalemba kuti: “ ‘Mwala umene omanga nyumba anawukana, womwewo wasanduka mwala wofunika kwambiri wa pa ngodya. Ambuye wachita izi, ndipo ndi zodabwitsa mʼmaso mwathu.’ Onani mutuwo |