Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 17:25 - Buku Lopatulika

25 Iye anavomera, Apereka. Ndipo polowa iye m'nyumba, Yesu anatsogola kunena naye, nati, Simoni, uganiza bwanji? Mafumu a dziko lapansi alandira msonkho kwa yani? Kwa ana ao kodi, kapena kwa akunja?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

25 Iye anavomera, Apereka. Ndipo polowa iye m'nyumba, Yesu anatsogola kunena naye, nati, Simoni, uganiza bwanji? Mafumu a dziko lapansi alandira msonkho kwa yani? Kwa ana ao kodi, kapena kwa akunja?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

25 Iye adati, “Amakhoma.” Tsono Petro ataloŵa m'nyumba, asananene chilichonse, Yesu adamufunsa kuti, “Iwe Simoni, ukuganiza bwanji? Kodi mafumu apansipano amalandira msonkho kwa yani? Kwa anthu a mtundu wao, kapena kwa alendo?”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

25 Iye anayankha kuti, “Inde amapereka.” Petro atalowa mʼnyumba, Yesu ndiye anayamba kuyankhula. Ndipo anamufunsa kuti, “Ukuganiza bwanji Simoni, kodi mafumu a dziko lapansi amalandira msonkho kuchokera kwa ana awo kapena kwa ena?”

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 17:25
8 Mawu Ofanana  

Ndipo m'mene iye anati, Kwa akunja, Yesu ananena kwa iye, Chifukwa chake anawo ali aufulu.


Chifukwa chake mutiuze ife, muganiza chiyani? Kuloledwa kodi kupatsa msonkho kwa Kaisara, kapena iai?


Tandionetsani Ine ndalama yamsonkho. Ndipo iwo anadza nalo kwa Iye rupiya latheka.


Nanena iwo, Cha Kaisara. Pomwepo Iye anati kwa iwo, Chifukwa chake patsani kwa Kaisara zake za Kaisara, ndi kwa Mulungu zake za Mulungu.


Koma Yesu anayankha, nati kwa iye, Balola tsopano: pakuti kuyenera ife kukwaniritsa chilungamo chonse motero. Pamenepo anamlola Iye.


kodi kuloledwa kupereka msonkho kwa Kaisara, kapena iai?


Nati Aisraele, Kodi mwaona munthu uyu amene anakwera kuno? Zoonadi iye anakwera kuti adzanyoze Israele, ndipo munthu wakumupha iye, mfumu idzamlemeretsa ndi chuma chambiri, nidzampatsa mwana wake wamkazi, nidzayesa nyumba ya atate wake yaufulu mu Israele.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa