Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 16:19 - Buku Lopatulika

19 Ndidzakupatsa mafungulo a Ufumu wa Kumwamba; ndipo chimene ukamanga padziko lapansi chidzakhala chomangidwa Kumwamba: ndipo chimene ukachimasula padziko lapansi, chidzakhala chomasulidwa Kumwamba.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

19 Ndidzakupatsa mafungulo a Ufumu wa Kumwamba; ndipo chimene ukamanga pa dziko lapansi chidzakhala chomangidwa Kumwamba: ndipo chimene ukachimasula pa dziko lapansi, chidzakhala chomasulidwa Kumwamba.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

19 Ndidzakupatsa makiyi a Ufumu wakumwamba, kotero kuti zimene udzamange pansi pano, zidzamangidwa ndi Kumwamba komwe, ndipo zimene udzamasule pansi pano, zidzamasulidwa ndi Kumwamba komwe.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

19 Ine ndidzakupatsa makiyi a Ufumu wakumwamba, ndipo chilichonse chimene iwe udzachimanga pansi pano chidzamangidwanso kumwamba.”

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 16:19
14 Mawu Ofanana  

Ndipo ndidzaika mfungulo wa nyumba ya Davide paphewa pake, ndipo iye adzatsegula, ndipo palibe wina adzatseka, iye adzatseka ndipo palibe wina adzatsegula.


Indetu ndinena kwa inu, Zilizonse mukazimanga padziko lapansi zidzakhala zomangidwa Kumwamba: ndipo zilizonse mukazimasula padziko lapansi, zidzakhala zomasulidwa Kumwamba.


Zochimwa za anthu ali onse muwakhululukira, zikhululukidwa kwa iwo; za iwo amene muzigwiritsa, zagwiritsidwa.


Ndipo pamene panali mafunsano ambiri, Petro anaimirira, nati kwa iwo, Abale, mudziwa kuti poyamba Mulungu anasankha mwa inu, kuti m'kamwa mwanga amitundu amve mau a Uthenga Wabwino, nakhulupirire.


Koma amene mumkhululukira kanthu, inenso nditero naye; pakuti chimene ndakhululukira inenso, ngati ndakhululukira kanthu, ndachichita chifukwa cha inu, pamaso pa Khristu;


Chifukwa chake iye wotaya ichi, sataya munthu, komatu Mulungu, wakupatsa Mzimu wake Woyera kwa inu.


ndi Wamoyoyo; ndipo ndinali wakufa, ndipo taona, ndili wamoyo kufikira nthawi za nthawi, ndipo ndili nazo zofungulira za imfa ndi dziko la akufa.


Izo zili nao ulamuliro wakutseka m'mwamba, isagwe mvula masiku a chinenero chao; ndipo ulamuliro zili nao pamadzi kuwasandutsa mwazi, ndi kupanda dziko ndi mliri uliwonse nthawi iliyonse zikafuna.


Ndipo kwa mngelo wa Mpingo wa ku Filadelfiya lemba: Izi anena Iye amene ali Woyera, Iye amene ali Woona, Iye wakukhala nacho chifungulo cha Davide, Iye wotsegula, ndipo palibe wina atseka; Iye wotseka, ndipo palibe wina atsegula:


Ndipo mngelo wachisanu anaomba lipenga, ndipo ndinaona nyenyezi yochokera kumwamba idagwa padziko; ndipo anampatsa iye chifunguliro cha chiphompho chakuya.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa