Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 11:30 - Buku Lopatulika

30 Pakuti goli langa lili lofewa, ndi katundu wanga ali wopepuka.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

30 Pakuti goli langa lili lofewa, ndi katundu wanga ali wopepuka.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

30 Pajatu goli limene ndimakoleka Ine nlosavuta, ndipo katundu amene ndimasenzetsa Ine ngwopepuka.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

30 Pakuti goli langa ndi losavuta ndipo katundu wanga ndi wopepuka.”

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 11:30
13 Mawu Ofanana  

Njira zake zili zokondweretsa, mayendedwe ake onse ndiwo mtendere.


Iye anakuuza, munthuwe, chomwe chili chokoma; ndipo Yehova afunanji nawe koma kuti uchite cholungama, ndi kukonda chifundo ndi kuyenda modzichepetsa ndi Mulungu wako.


Nyengo imeneyo Yesu anapita tsiku la Sabata pakati pa minda ya tirigu; ndipo ophunzira ake anali ndi njala, nayamba kubudula ngala, nadya.


Zinthu izi ndalankhula ndi inu, kuti mwa Ine mukakhale nao mtendere. M'dziko lapansi mudzakhala nacho chivuto, koma limbikani mtima; ndalingonjetsa dziko lapansi Ine.


Nanga bwanji tsopano mulikumuyesa Mulungu, kuti muike pa khosi la ophunzira goli, limene sanathe kunyamula kapena makolo athu kapena ife?


Pakuti chinakomera Mzimu Woyera ndi ife, kuti tisasenzetse inu chothodwetsa chachikulu china choposa izi zoyenerazi;


Pakuti chisautso chathu chopepuka cha kanthawi chitichitira ife kulemera koposa kwakukulu ndi kosatha kwa ulemerero;


Khristu anatisandutsa mfulu, kuti tikhale mfulu; chifukwa chake chilimikani, musakodwenso ndi goli la ukapolo.


Ngati Mzimu akutsogolerani, simuli omvera lamulo.


Ndikhoza zonse mwa Iye wondipatsa mphamvuyo.


Pakuti ichi ndi chikondi cha Mulungu, kuti tisunge malamulo ake: ndipo malamulo ake sali olemetsa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa