Marko 9:18 - Buku Lopatulika18 ndipo ponse pamene umgwira, umgwetsa; ndipo achita thovu, nakukuta mano, nanyololoka; ndipo ndinalankhula nao ophunzira anu kuti autulutse; koma sanakhoze. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201418 ndipo ponse pamene umgwira, umgwetsa; ndipo achita thovu, nakukuta mano, nanyololoka; ndipo ndinalankhula nao ophunzira anu kuti autulutse; koma sanakhoze. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa18 Umati ukangomugwira, umamgwetsa pansi, mwanayo nkumangoti thovu tututu kukamwa, namakukuta mano, mpaka thupi gwagwagwa kuuma. Ndiye ndinapempha ophunzira anuŵa kuti autulutse, koma alephera.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero18 Nthawi iliyonse ukamugwira umamugwetsa pansi. Amatuluka thovu kukamwa, amakukuta mano ake ndipo amawuma. Ndinapempha ophunzira anu kuti awutulutse mzimuwo, koma sanathe.” Onani mutuwo |