Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Malaki 2:9 - Buku Lopatulika

9 Chifukwa chake Inenso ndakuikani onyozeka ndi ochepseka kwa anthu onse, popeza simunasunge njira zanga, koma munaweruza mwankhope pochita chilamulo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Chifukwa chake Inenso ndakuikani onyozeka ndi ochepseka kwa anthu onse, popeza simunasunga njira zanga, koma munaweruza mwankhope pochita chilamulo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Nchifukwa chake Inenso ndakusandutsani onyozeka ndi achabechabe pamaso pa anthu, popeza kuti simudatsate njira zanga, ndipo mwakhala mukukondera poweruza milandu.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 “Choncho Ine ndachititsa kuti munyozedwe ndi kuchititsidwa manyazi pamaso pa anthu onse, chifukwa simunatsate njira zanga koma mwakhala mukuonetsa kukondera pa nkhani za malamulo.”

Onani mutuwo Koperani




Malaki 2:9
30 Mawu Ofanana  

Ndipo Mikaya anati, Mukabwera ndithu ndi mtendere Yehova sanalankhule mwa ine. Nati, Mvetsani, anthu inu nonse.


Ndisati ndisamalire nkhope ya munthu, kapena kumtchula munthu maina omdyola nao;


Amayesa wolungama wodala pomkumbukira; koma dzina la oipa lidzavunda.


Munthu amatamandidwa monga mwa nzeru yake; koma wokhota mtima adzanyozedwa.


Zokuta mitu zanu zomwe ndidzazing'amba, ndi kulanditsa anthu anga m'manja mwanu; ndipo sadzakhalanso m'mphamvu mwanu kusakidwa; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.


Lidzafika tsoka lotsatanatsatana, kudzakhalanso mbiri yotsatanatsatana, ndipo adzafunafuna masomphenya a mneneri, koma malamulo adzatayikira wansembe, uphungu ndi kutayikira akulu.


Akulu ake aweruza chifukwa cha mphotho, ndi ansembe ake aphunzitsa chifukwa cha malipo, ndi aneneri ake alosa chifukwa cha ndalama; koma atsamira pa Yehova, nati, Kodi Yehova sali pakati pa ife? Palibe choipa chodzatigwera.


Ndipo ndidzakuponyera zonyansa, ndi kukuchititsa manyazi, ndi kukuika chopenyapo.


Taonani, ndidzaipsa mbeu chifukwa cha inu, ndi kuwaza ndowe pankhope panu, ndizo ndowe za nsembe zanu, ndipo adzakuchotsani pamodzi nacho.


Koma inu mwapatuka m'njira; mwakhumudwitsa ambiri m'chilamulo; mwaipsa chipangano cha Levi, ati Yehova wa makamu.


Koma iye, pofuna kudziyesa yekha wolungama, anati kwa Yesu, Ndipo mnansi wanga ndani?


Koma tsoka inu, Afarisi! Chifukwa mupereka limodzi la magawo khumi la timbeu tonunkhira, ndi timbeu tokometsa chakudya ndi ndiwo zonse, ndipo mumaleka chiweruzo ndi chikondi cha Mulungu; mwenzi mutachita izi, ndi kusasiya zinazo.


Koma iwo akuyesedwa ali kanthu (ngati anali otani kale, kulibe kanthu kwa ine; Mulungu salandira nkhope ya munthu) iwo omvekawo sanandionjezere ine kanthu;


Musamasamalira munthu poweruza mlandu; ang'ono ndi akulu muwamvere chimodzimodzi; musamaopa nkhope ya munthu; popeza chiweruzo ncha Mulungu; ndipo mlandu ukakukanikani mubwere nao kwa ine, ndidzaumva.


Chifukwa chake Yehova Mulungu wa Israele akuti, Ndinaterodi kuti banja lako ndi banja la kholo lako lidzayenda pamaso panga nthawi zonse; koma tsopano Yehova ati, Chikhale kutali ndi Ine; popeza amene andilemekeza Ine, Inenso ndidzawalemekeza iwowa, ndipo akundipeputsa Ine, adzapeputsidwa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa