Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Malaki 2:6 - Buku Lopatulika

6 Chilamulo cha zoona chinali m'kamwa mwake, ndi chosalungama sichinapezeke m'milomo mwake; anayenda nane mumtendere ndi moongoka, nabweza ambiri aleke mphulupulu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Chilamulo cha zoona chinali m'kamwa mwake, ndi chosalungama sichinapezeka m'milomo mwake; anayenda nane mumtendere ndi moongoka, nabweza ambiri aleke mphulupulu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Malangizo amene ankapereka anali oona, pakamwa pao sipankatuluka zosalungama. Ankamvana nane, ndipo ankayenda mokhulupirika ndi Ine, motero ankabweza anthu ambiri m'njira zao zoipa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Pakamwa pake pankatuluka malangizo woona, ndipo pa milomo yake sipanapezeke chinyengo. Iye anayenda nane mwamtendere ndi molungama mtima, ndipo anabweza anthu ambiri mʼnjira zawo zauchimo.

Onani mutuwo Koperani




Malaki 2:6
27 Mawu Ofanana  

Pamene Abramu anali wa zaka makumi asanu ndi anai kudza zisanu ndi zinai, Yehova anamuonekera Abramu nati kwa iye, Ine ndine Mulungu Wamphamvuyonse; yenda iwe pamaso panga, nukhale wangwiro.


Mibadwo ya Nowa ndi iyi: Nowa anali munthu wolungama ndi wangwiro m'mibadwo yake; Nowa anayendabe ndi Mulungu.


Chilungamo chanu ndicho chilungamo chosatha; ndi chilamulo chanu ndicho choonadi.


Inu muli pafupi, Yehova; ndipo malamulo anu onse ndiwo choonadi.


Pakamwa pa wolungama palankhula zanzeru, ndi lilime lake linena chiweruzo.


Tapenya wangwiro, ndipo taona woongoka mtima! Pakuti ku matsiriziro ake a munthuyo kuli mtendere.


ukasunge zolingalira, milomo yako ilabadire zomwe udziwa.


Koma akadaima mu upo wanga, akadamvetsa anthu anga mau anga, akadatembenuza iwo kunjira yao yoipa, ndi kuchoipa cha ntchito zao.


Ndipo aphunzitsi adzawala ngati kunyezimira kwa thambo; ndi iwo otembenuza ambiri atsate chilungamo ngati nyenyezi kunthawi za nthawi.


Anthu anga aonongeka chifukwa cha kusadziwa; popeza unakana kudziwa, Inenso ndikukaniza, kuti usakhale wansembe wanga; popeza waiwala chilamulo cha Mulungu wako, Inenso ndidzaiwala ana ako.


Ndipo anatumiza kwa Iye ophunzira ao, pamodzi ndi Aherode, amene ananena, Mphunzitsi, tidziwa kuti muli woona, ndipo muphunzitsa njira ya Mulungu moona ndithu, ndipo simusamala munthu aliyense; pakuti simuyang'anira pa nkhope ya anthu.


Ndipo pamene anafika, ananena naye, Mphunzitsi, tidziwa kuti muli woona, ndipo simusamala munthu; pakuti simuyang'ana nkhope ya anthu, koma muphunzitsa njira ya Mulungu moona: Nkuloleka kodi kupereka msonkho kwa Kaisara, kapena iai?


Ndipo onse awiri anali olungama mtima pamaso pa Mulungu, namayendabe m'malamulo onse ndi zoikika za Ambuye osachimwa.


Ndipo anamfunsa Iye, nanena, Mphunzitsi, ife tidziwa kuti munena ndi kuphunzitsa kolunjika, ndi kusasamalira nkhope ya munthu, koma muphunzitsa njira ya Mulungu koonadi;


kukawatsegulira maso ao, kuti atembenuke kuchokera kumdima, kulinga kukuunika, ndi kuchokera ulamuliro wa Satana kulinga kwa Mulungu, kuti alandire iwo chikhululukiro cha machimo, ndi cholowa mwa iwo akuyeretsedwa ndi chikhulupiriro cha mwa Ine.


Adzaphunzitsa Yakobo maweruzo anu, ndi Israele chilamulo chanu; adzaika chofukiza pamaso panu, ndi nsembe yopsereza yamphumphu paguwa la nsembe lanu.


Ndipo za Levi anati, Tumimu ndi Urimu wanu zikhala ndi wokondedwa wanu, amene mudamuyesa mu Masa, amene mudalimbana naye ku madzi a Meriba;


amene anati za atate wake ndi amai wake, sindinamuone; Sanazindikire abale ake, sanadziwe ana ake omwe; popeza anasamalira mau anu, nasunga chipangano chanu.


Ndipo m'kamwa mwao simunapezedwe bodza; ali opanda chilema.


Koma ana a Eli anali oipa; sanadziwe Yehova.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa