Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Malaki 2:3 - Buku Lopatulika

3 Taonani, ndidzaipsa mbeu chifukwa cha inu, ndi kuwaza ndowe pankhope panu, ndizo ndowe za nsembe zanu, ndipo adzakuchotsani pamodzi nacho.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Taonani, ndidzaipsa mbeu chifukwa cha inu, ndi kuwaza ndowe pankhope panu, ndizo ndowe za nsembe zanu, ndipo adzakuchotsani pamodzi nacho.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 “Ndidzalanga zidzukulu zanu. Ndidzakupakani ndoŵe za nsembe zanu kumaso, ndipo ndidzakutayani ku nkhuti ya ndoŵe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 “Ine ndidzalanga zidzukulu zanu chifukwa cha inu; ndidzakupakani kumaso ndowe za nsembe zanu zachikondwerero, ndipo ndidzakutayani pamodzi ndi ndowezo.”

Onani mutuwo Koperani




Malaki 2:3
16 Mawu Ofanana  

chifukwa chake, taona ndidzafikitsa choipa pa nyumba ya Yerobowamu, ndi kugulula mwana wamwamuna yense wa Yerobowamu womangika ndi womasuka mu Israele, ndipo ndidzachotsa psiti nyumba yonse ya Yerobowamu, monga munthu achotsa ndowe kufikira idatha yonse.


koma adzatayika kosatha ngati zonyansa zake; iwo amene adamuona adzati, Ali kuti iye?


Mulungu wakwera ndi mfuu, Yehova ndi liu la lipenga.


amene anaonongeka ku Endori; anakhala ngati ndowe ya kumunda.


Koma nyama ya ng'ombeyo, ndi chikopa chake, ndi chipwidza chake, uzitentha izi ndi moto kunja kwa chigono; ndiyo nsembe yauchimo.


ndipo udzawayanika padzuwa, ndi pamwezi, ndi pa khamu lonse la kuthambo, limene analikonda, ndi kulitumikira, ndi kulitsata, ndi kulifuna, ndi kuligwadira; sadzasonkhanidwa, sadzaikidwa; adzakhala ndowe panthaka.


M'munda mwaonongeka, nthaka ilira; pakuti tirigu waonongeka, vinyo watsopano wamwelera, mafuta akudza pang'onong'ono.


Mbeu zaola pansi pa zibuluma zao; zosungiramo zaonongeka, nkhokwe zapasuka; pakuti tirigu wakwinyata.


ndidzachitira inu ichinso; ndidzakuikirani zoopsa, nthenda yoondetsa ya m'chifuwa ndi malungo, zakulanda maso ndi mphamvu, ndi kuzunza moyo; ndipo mudzabzala mbeu zanu chabe, popeza adani anu adzazidya.


Ndipo ndidzakuponyera zonyansa, ndi kukuchititsa manyazi, ndi kukuika chopenyapo.


Chifukwa chake Inenso ndakuikani onyozeka ndi ochepseka kwa anthu onse, popeza simunasunge njira zanga, koma munaweruza mwankhope pochita chilamulo.


Suyenera kuuthira pamunda kapena padzala, autaya kunja. Amene ali nao makutu akumva amve.


ponamizidwa, tipempha; takhala monga zonyansa za dziko lapansi, litsiro la zinthu zonse, kufikira tsopano.


Mudzatuluka nazo mbeu zambiri kumunda, koma mudzakolola pang'ono; popeza dzombe lidzazitha.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa