Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 6:4 - Buku Lopatulika

4 Koma ife tidzalimbika m'kupemphera, ndi kutumikira mau.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Koma ife tidzalimbika m'kupemphera, ndi kutumikira mau.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Koma ife tidzadzipereka ku ntchito ya kupemphera ndi kulalika mau a Mulungu.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Koma ife tidzadzipereka kuti tizipemphera ndi kulalikira mawu.”

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 6:4
18 Mawu Ofanana  

Ndipo kunali, pamene masiku a utumiki wake anamalizidwa, anamuka kunyumba kwake.


Iwo onse analikukangalika m'kupemphera, pamodzi ndi akazi, ndi Maria, amake wa Yesu, ndi abale ake omwe.


Ndipo anali chikhalire m'chiphunzitso cha atumwi ndi m'chiyanjano, m'kunyema mkate ndi mapemphero.


Pakuti Mulungu ali mboni yanga, amene ndimtumikira mu mzimu wanga, mu Uthenga Wabwino wa Mwana wake, kuti kosalekeza ndikumbukira inu,


Pakuti ngati ndilalikira Uthenga Wabwino ndilibe kanthu kakudzitamandira; pakuti chondikakamiza ndigwidwa nacho; pakuti tsoka ine ngati sindilalikira Uthenga Wabwino.


nthawi zonse m'pembedzero langa lonse la kwa inu nonse ndichita pembedzerolo ndi kukondwera,


Pakuti ndifuna kuti inu mudziwe nkhawa imene ndili nayo chifukwa cha inu, ndi iwowa a mu Laodikea, ndi onse amene sanaone nkhope yanga m'thupi;


Akupatsani moni Epafra ndiye wa kwa inu, ndiye kapolo wa Khristu Yesu, wakulimbika m'mapemphero ake masiku onse chifukwa cha inu, kuti mukaime amphumphu ndi odzazidwa m'chifuniro chonse cha Mulungu.


Ndipo nenani kwa Arkipo, Samaliratu utumiki umene udaulandira mwa Ambuye, kuti uukwanitse.


lalikira mau; chita nao pa nthawi yake, popanda nthawi yake; tsutsa, dzudzula, chenjeza, ndi kuleza mtima konse ndi chiphunzitso.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa