Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 17:3 - Buku Lopatulika

3 natsimikiza, kuti kunayenera Khristu kumva zowawa, ndi kuuka kwa akufa; ndiponso kuti Yesu yemweyo, amene ndikulalikirani inu, ndiye Khristu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 natsimikiza, kuti kunayenera Khristu kumva zowawa, ndi kuuka kwa akufa; ndiponso kuti Yesu yemweyo, amene ndikulalikirani inu, ndiye Khristu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Adaŵamasulira za m'Malembomo ndi kuŵatsimikizira kuti Mpulumutsi wolonjezedwa uja adaayenera kumva zoŵaŵa kenaka nkuuka kwa akufa. Paulo adati, “Yesu amene ndikukulalikiraniyu, ndiye Mpulumutsiyo.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 kuwafotokozera ndi kuwatsimikizira kuti Khristu anayenera kufa ndi kuuka. Iye anati, “Yesu amene ndikukulalikirani ndiye Khristu.”

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 17:3
16 Mawu Ofanana  

Ndipo anati wina kwa mnzake, Mtima wathu sunali wotentha m'kati mwathu nanga m'mene analankhula nafe m'njira, m'mene anatitsegulira malembo?


Ndipo anati kwa iwo, Awa ndi mauwo ndinalankhula nanu, paja ndinakhala ndi inu, kuti ziyenera kukwanitsidwa zonse zolembedwa za Ine m'chilamulo cha Mose, ndi aneneri, ndi Masalimo.


ndipo anati kwa iwo, Kotero kwalembedwa, kuti Khristu amve zowawa, nauke kwa akufa tsiku lachitatu;


Pakuti kufikira pomwepo sanadziwe lembo lakuti ayenera Iye kuuka kwa akufa.


ndipo posonkhana nao pamodzi, anawalamulira asachoke ku Yerusalemu, komatu alindire lonjezano la Atate, limene, anati, munalimva kwa Ine;


pakuti ndi mphamvu anatsutsa Ayuda, pamaso pa anthu, nasonyeza mwa malembo kuti Yesu ndiye Khristu.


Koma pamene Silasi ndi Timoteo anadza potsika ku Masedoniya, Paulo anapsinjidwa ndi mau, nachitira umboni kwa Ayuda kuti Yesu ndiye Khristu.


Koma zimene Mulungu analalikiratu m'kamwa mwa aneneri onse, kuti adzamva kuwawa Khristu, Iye anakwaniritsa chotero.


Koma Saulo anakula makamaka mumphamvu, nadodometsa Ayuda akukhala mu Damasiko, nawatsimikizira kuti ameneyo ndi Khristu.


Agalatiya opusa inu, anakulodzani ndani, inu amene Yesu Khristu anaonetsedwa pamaso panu, wopachikidwa?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa