Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 13:34 - Buku Lopatulika

34 Ndipo kuti anamuukitsa Iye kwa akufa, wosabweranso kuchivundi, anateropo, Ndidzakupatsani inu madalitso oyera ndi okhulupirika a Davide.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

34 Ndipo kuti anamuukitsa Iye kwa akufa, wosabweranso kuchivundi, anateropo, Ndidzakupatsani inu madalitso oyera ndi okhulupirika a Davide.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

34 Ndipo zakuti adamuukitsa kwa akufa kuti asaole konse, Mulungu adati, ‘Ndidzakupatsani madalitso opatulika ndi okhulupirika amene ndidalonjeza Davide.’

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

34 Zakuti Mulungu anamuukitsa kuti asawole konse, zinanenedwa mʼmawu awa: “ ‘Ine, ndidzakupatsa madalitso opatulika ndi odalirika amene ndinalonjeza Davide.’

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 13:34
18 Mawu Ofanana  

Zoonadi nyumba yanga siikhala yotere ndi Mulungu; koma Iye anapangana ndi ine pangano losatha, lolongosoka mwa zonse ndi losungika; pakuti ichi ndi chipulumutso changa chonse, ndi kufuma kwanga konse, kodi sadzachimeretsa?


Tcherani khutu lanu, mudze kwa Ine, imvani, mzimu wanu nudzakhala ndi moyo; ndipo ndidzapangana nanu chipangano chosatha, ndicho zifundo zoona za Davide.


koma adzamtumikira Yehova Mulungu wao, ndi Davide mfumu yao, imene Ndidzawaukitsira.


pamenepo ndidzatayanso mbeu ya Yakobo, ndi ya Davide mtumiki wanga, kuti sindidzatenganso za mbeu zake kuti zikhale zolamulira mbeu za Abrahamu, ndi za Isaki, ndi za Yakobo; pakuti ndidzabweza undende wao, ndipo ndidzawachitira chifundo.


atatero ana a Israele adzabwera, nadzafuna Yehova Mulungu wao, ndi Davide mfumu yao, nadzafika ndi mantha kwa Yehova, ndi ku ukoma wake masiku otsiriza.


Tsiku lomwelo ndidzautsa msasa wa Davide udagwawo, ndi kukonzanso zopasuka zake; ndipo ndidzautsa zogumuka zake, ndi kuumanga monga masiku a kalelo;


Tsiku ilo Yehova adzatchinjiriza okhala mu Yerusalemu; ndi iye wokhumudwa pakati pao tsiku lomwelo adzakhala ngati Davide; ndi nyumba ya Davide idzakhala ngati Mulungu, ngati mthenga wa Yehova pakati pao.


Koma Mulungu anamuukitsa Iye kwa akufa;


kuti Mulungu analikwaniritsa ili kwa ana athu pakuukitsa Yesu; monganso mulembedwa mu Salimo lachiwiri, Iwe ndiwe Mwana wanga, lero ndakubala.


koma Iye amene Mulungu anamuukitsa sanaone chivundi.


yemweyo Mulungu anamuukitsa, atamasula zowawa za imfa, mwakuti sikunali kotheka kuti Iye agwidwe nayo.


podziwa kuti Khristu anaukitsidwa kwa akufa, sadzafanso; imfa siichitanso ufumu pa Iye.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa