Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 12:4 - Buku Lopatulika

4 Ndipo m'mene adamgwira, anamuika m'ndende, nampereka kwa magulu anai a alonda, lonse anaianai, amdikire iye; ndipo anafuna kumtulutsa kudza naye kwa anthu atapita Paska.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Ndipo m'mene adamgwira, anamuika m'ndende, nampereka kwa magulu anai a alonda, lonse anaianai, amdikire iye; ndipo anafuna kumtulutsa kudza naye kwa anthu atapita Paska.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Atamgwira, adamtsekera m'ndende, nampereka kwa magulu anai a asilikali kuti azimlonda, gulu lililonse asilikali anai. Tsono Herode ankafuna kuzenga mlandu wake pamaso pa anthu onse, chikondwerero cha Paska chitapita.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Atamugwira Petro, namutsekera mʼndende, anamupereka kwa magulu anayi a asilikali kuti amuyangʼanire, gulu lililonse linali ndi asilikali anayi. Herode anafuna kumuzenga mlandu pamaso pa anthu onse chikondwerero cha Paska chitapita.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 12:4
22 Mawu Ofanana  

Ndipo anatumiza makalata ndi amtokoma kumaiko onse a mfumu, kuti aononge, aphe, napulule Ayuda onse, ndiwo ana, ndi okalamba, makanda, ndi akazi, tsiku limodzi, ndilo tsiku lakhumi ndi chitatu la mwezi wakhumi ndi chiwiri, ndiwo mwezi wa Adara; nalande zao mofunkha.


Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni m'dziko la Ejipito, ndi kuti,


Muli zolingalira zambiri m'mtima mwa munthu; koma uphungu wa Yehova ndiwo udzaimika.


Usanyadire zamawa, popeza sudziwa tsiku lina lidzabala chiyani?


Ndani anganene, chonena chake ndi kuchitikadi, ngati Ambuye salamulira?


Pamenepo adzakuperekani kunsautso, nadzakuphani; ndipo anthu a mitundu yonse adzadana nanu, chifukwa cha dzina langa.


Koma ananena iwo, pa nthawi ya chikondwerero iai, kuti pasakhale phokoso la anthu.


Ndipo popita masiku awiri kuli phwando la Paska ndi Mkate wopanda chotupitsa; ndipo ansembe aakulu ndi alembi anafunafuna momchitira chiwembu, ndi kumupha:


Koma zisanachitike izi, anthu adzakuthirani manja, nadzakuzunzani, nadzapereka inu ku masunagoge ndi ndende, nadzamuka nanu kwa mafumu ndi akazembe, chifukwa cha dzina langa.


Ndipo anati kwa Iye, Ambuye, ndilipo ndikapite ndi Inu kundende ndi kuimfa.


Pamenepo asilikali, m'mene adapachika Yesu, anatenga zovala zake, anadula panai, natenga wina china, wina china, ndiponso malaya; koma malaya anaombedwa monsemo kuyambira pamwamba pake, analibe msoko.


Indetu, indetu, ndinena ndi iwe, pamene unali mnyamata unadzimangira wekha m'chuuno, ndipo unayenda kumene unafuna; koma pamene udzakalamba udzatulutsa manja ako, ndipo adzakumanga wina, nadzakunyamula kumene sufuna.


Ndipo pakuona kuti kudakondweretsa Ayuda, anaonjezapo nagwiranso Petro. Ndipo awo ndi masiku a mkate wopanda chotupitsa.


Pamenepo ndipo Petro anasungika m'ndende; koma Mpingo anampempherera iye kwa Mulungu kosalekeza.


kuti achite zilizonse dzanja lanu ndi uphungu wanu zidaweruziratu zichitike.


Ndipo anawathira manja, nawaika m'ndende kufikira m'mawa; pakuti mpa madzulo pamenepo.


nathira manja atumwi, nawaika m'ndende ya anthu wamba.


Ndipo Saulo anapasula Mpingo, nalowa nyumba ndi nyumba, nakokamo amuna ndi akazi, nawaika m'ndende.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa