Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 8:16 - Buku Lopatulika

16 Ndipo palibe munthu atayatsa nyali, aivundikira ndi chotengera, kapena kuiika pansi pa kama; koma aiika pa choikapo, kuti iwo akulowamo aone kuunikaku.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Ndipo palibe munthu atayatsa nyali, aivundikira ndi chotengera, kapena kuiika pansi pa kama; koma aiika pa choikapo, kuti iwo akulowamo aone kuunikaku.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 “Palibe munthu amene amayatsa nyale nkuivundikira ndi mbiya, kapena kuibisa kunsi kwa bedi. Koma amaiika pa malo oonekera, kuti anthu oloŵa m'nyumba aone kuŵala kwake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 “Palibe amayatsa nyale ndi kuyibisa mu mtsuko kapena kuyika pansi pa bedi. Koma mʼmalo mwake, amayika pa choyikapo chake, kuti anthu olowamo aone kuwala.

Onani mutuwo Koperani




Luka 8:16
9 Mawu Ofanana  

Palibe munthu, atayatsa nyali, aiika m'chipinda chapansi, kapena pansi pa mbiya, koma pa choikapo chake, kuti iwo akulowamo aone kuunika.


Ndipo zija za m'nthaka yokoma, ndiwo amene anamva mau nawasunga mu mtima woona ndi wabwino, nabala zipatso ndi kupirira.


kukawatsegulira maso ao, kuti atembenuke kuchokera kumdima, kulinga kukuunika, ndi kuchokera ulamuliro wa Satana kulinga kwa Mulungu, kuti alandire iwo chikhululukiro cha machimo, ndi cholowa mwa iwo akuyeretsedwa ndi chikhulupiriro cha mwa Ine.


chinsinsi cha nyenyezi zisanu ndi ziwiri zimene unaziona padzanja langa lamanja, ndi zoikaponyali zisanu ndi ziwiri zagolide: nyenyezi zisanu ndi ziwiri ndizo angelo a Mipingo isanu ndi iwiri; ndipo zoikaponyali zisanu ndi ziwiri ndizo Mipingo isanu ndi iwiri.


Izo ndizo mitengo iwiri ya azitona ndi zoikaponyali ziwiri zakuima pamaso pa Ambuye wa dziko lapansi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa