Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 8:12 - Buku Lopatulika

12 Ndipo za m'mbali mwa njira ndiwo anthu amene adamva; pamenepo akudza mdierekezi, nachotsa mau m'mitima yao, kuti angakhulupirire ndi kupulumuka.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Ndipo za m'mbali mwa njira ndiwo anthu amene adamva; pamenepo akudza mdierekezi, nachotsa mau m'mitima yao, kuti angakhulupirire ndi kupulumuka.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Mbeu zogwera m'njira zija zikutanthauza anthu amene amaŵamva mau a Mulungu. Koma Satana amabwera, nkuchotsa mau aja m'mitima mwao, kuwopa kuti angakhulupirire ndi kupulumuka.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Mbewu za mʼmbali mwa njira ndi anthu amene amamva mawu, ndipo kenaka mdierekezi amabwera ndi kuchotsa mawuwo mʼmitima mwawo kuti asakhulupirire ndi kupulumutsidwa.

Onani mutuwo Koperani




Luka 8:12
13 Mawu Ofanana  

chifukwa anada nzeru, sanafune kuopa Yehova;


Tenga nzeru, tenga luntha; usaiwale, usapatuke pa mau a m'kamwa mwanga;


Koma inu amene mwasiya Yehova, amene mwaiwala phiri langa lopatulika, ndi kukonzera mulungu wamwai gome, ndi kudzazira mulungu waimfa zikho za vinyo wosakaniza;


Munthu aliyense wakumva mau a Ufumu, osawadziwitsai, woipayo angodza, nakwatula chofesedwacho mumtima mwake. Uyo ndiye wofesedwa m'mbali mwa njira.


Ndipo m'kufesa kwake zina zinagwa m'mbali mwa njira, ndipo zinadza mbalame, nkulusira izo.


Ndipo iwo ndiwo a m'mbali mwa njira mofesedwamo mau; ndipo pamene anamva, pomwepo akudza Satana nachotsa mau ofesedwa mwa iwo.


Koma fanizoli litere: Mbeuzo ndizo mau a Mulungu.


Ndipo za pathanthwe ndiwo amene, pakumva, alandira mau ndi kukondwera; koma alibe mizu; akhulupirira kanthawi, ndipo pa nthawi ya mayesedwe angopatuka.


Anatuluka wofesa kukafesa mbeu zake; ndipo m'kufesa kwake zina zinagwa m'mbali mwa njira; ndipo zinapondedwa, ndi mbalame za m'mlengalenga zinatha kuzidya.


Ndipo chinaponyedwa pansi chinjoka chachikulu, njoka yokalambayo, iye wotchedwa mdierekezi ndi Satana, wonyenga wa dziko lonse; chinaponyedwa pansi kudziko, ndi angelo ake anaponyedwa naye pamodzi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa