Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 4:35 - Buku Lopatulika

35 Ndipo Yesu anamdzudzula iye, nanena, Tonthola, nutuluke mwa iye. Ndipo chiwandacho m'mene chinamgwetsa iye pakati, chinatuluka mwa iye chosampweteka konse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

35 Ndipo Yesu anamdzudzula iye, nanena, Tonthola, nutuluke mwa iye. Ndipo chiwandacho m'mene chinamgwetsa iye pakati, chinatuluka mwa iye chosamphweteka konse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

35 Koma Yesu adazazira mzimu woipawo, adati, “Khala chete, tuluka mwa munthuyu.” Apo mzimu womuipitsa uja udamugwetsa pansi munthuyo pakati pa anthu, nkutuluka, osamupweteka konse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

35 Yesu anachidzudzula kwambiri nati, “Khala chete! Tuluka mwa iye.” Chiwandacho chinamugwetsa munthuyo pansi pamaso pa onse ndipo chinatuluka wosamupweteka.

Onani mutuwo Koperani




Luka 4:35
17 Mawu Ofanana  

Koma kwa woipa Mulungu anena, Uli nao chiyani malemba anga kulalikira, ndi kutchula pangano langa pakamwa pako?


Ndipo Yehova anati kwa Satana, Yehova akudzudzula, Satana iwe; inde Yehova amene anasankha Yerusalemu akudzudzula; uyu sindiye muuni wofumulidwa kumoto?


Ndipo Yesu anamdzudzula; ndipo chiwanda chinatuluka mwa iye; ndipo mnyamatayo anachira kuyambira nthawi yomweyo.


Ndipo ananena Iye kwa iwo, Muli amantha bwanji, okhulupirira pang'ono inu? Pomwepo Iye anauka, nadzudzula mphepo ndi nyanja, ndipo panagwa bata lalikulu.


Ndipo mzimu wonyansa, pomng'amba, ndi kufuula ndi mau aakulu, unatuluka mwa iye.


Ndipo anauka, nadzudzula mphepo, nati kwa nyanja, kuti, Tonthola, khala bata. Ndipo mphepo inaleka, ndipo kunagwa bata lalikulu.


Ndipo pamene unafuula, numng'ambitsa, unatuluka; ndipo mwana anakhala ngati wakufa; kotero kuti ambiri ananena, Wamwalira.


koma pamene paliponse amdzera wakumposa mphamvu, nakamgonjetsa, amchotsera zida zake zonse zimene anazitama, nagawa zofunkha zake.


Ndipo anati kwa iwo, Kwenikweni mudzati kwa Ine nkhani iyi, Sing'anga iwe, tadzichiritsa wekha: zonse zija tazimva zinachitidwa ku Kapernao, muzichitenso zomwezo kwanu kuno.


Ndipo Iye anaimirira, naweramira pa iye, nadzudzula nthendayo; ndipo inamleka iye: ndipo anauka msangatu, nawatumikira.


Ndi ziwanda zomwe zinatuluka mwa ambiri, ndi kufuula, kuti, Inu ndinu Mwana wa Mulungu. Ndipo Iye anazidzudzula, wosazilola kulankhula, chifukwa zinamdziwa kuti Iye ndiye Khristu.


Ndipo anadza kwa Iye, namuutsa, nanena, Ambuye, Ambuye, titayika. Ndipo anauka, nadzudzula mphepo ndi mafunde ake a madzi; pomwepo zinaleka, ndipo panagwa bata.


ndipo onani, umamgwira iye mzimu, nafuula modzidzimuka; ndipo umamng'amba iye ndi kumchititsa thovu pakamwa, suchoka pa iye, koma umsautsa koopsa.


Ndipo akadadza iye, chiwandacho chinamgwetsa, ndi kumng'ambitsa. Koma Yesu anadzudzula mzimu wonyansawo, nachiritsa mnyamata, nambwezera iye kwa atate wake.


Chifukwa chake, kondwerani, miyamba inu, ndi inu akukhala momwemo. Tsoka mtunda ndi nyanja, chifukwa mdierekezi watsikira kwa inu, wokhala nao udani waukulu, podziwa kuti kamtsalira kanthawi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa