Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 24:6 - Buku Lopatulika

6 Palibe kuno Iye, komatu anauka; kumbukirani muja adalankhula nanu, pamene analinso mu Galileya,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Palibe kuno Iye, komatu anauka; kumbukirani muja adalankhula nanu, pamene analinso m'Galileya,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Sali muno ai, wauka. Kumbukirani zimene adaakuuzani akadali ku Galileya.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Iye sali muno ayi. Wauka! Kumbukirani zimene anakuwuzani pamene anali nanu ku Galileya:

Onani mutuwo Koperani




Luka 24:6
19 Mawu Ofanana  

pakuti monga Yona anali m'mimba mwa chinsomba masiku atatu ndi usiku wake, chomwecho Mwana wa Munthu adzakhala mumtima mwa dziko lapansi masiku atatu ndi usiku wake.


Kuyambira pamenepo Yesu anayamba kuwalangiza ophunzira ake, kuti kuyenera Iye amuke ku Yerusalemu, kukazunzidwa zambiri ndi akulu, ndi ansembe aakulu, ndi alembi; ndi kukaphedwa, ndi tsiku lachitatu kuuka kwa akufa.


nanena, Mfumu, takumbukira ife kuti wonyenga uja anati, pamene anali ndi moyo, Ndidzauka pofika masiku atatu.


Iye mulibe muno iai; pakuti anauka, monga ananena. Idzani muno mudzaone malo m'mene anagonamo Ambuye.


Ndipo iye ananena nao, Musadabwe: mulikufuna Yesu Mnazarene amene anapachikidwa; anauka; sali pano; taonani, mbuto m'mene anaikamo Iye!


Ndipo anayamba kuwaphunzitsa, kuti kuyenera kuti Mwana wa Munthu akamve zowawa zambiri, nakakanidwe ndi akulu ndi ansembe aakulu, ndi alembi, nakaphedwe, ndipo mkucha wake akauke.


nanena, Ambuye anauka ndithu, naonekera kwa Simoni.


ndipo m'mene anakhala ndi mantha naweramira pansi nkhope zao, anati kwa iwo, Mufuniranji wamoyo pa akufa?


nati, Kuyenera kuti Mwana wa Munthu amve zowawa zambiri, ndi kukanidwa ndi akulu, ndi ansembe aakulu, ndi alembi, ndi kuphedwa, ndi kuuka tsiku lachitatu.


Alowe mau amenewa m'makutu anu; pakuti Mwana wa Munthu adzaperekedwa m'manja a anthu.


yemweyo Mulungu anamuukitsa, atamasula zowawa za imfa, mwakuti sikunali kotheka kuti Iye agwidwe nayo.


Simukumbukira kodi, kuti pokhala nanu, ndisanachoke ine, ndinakuuzani izi?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa