Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 17:3 - Buku Lopatulika

3 Kadzichenjerani nokha; akachimwa mbale wako umdzudzule, akalapa, umkhululukire.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Kadzichenjerani nokha; akachimwa mbale wako umdzudzule, akalapa, umkhululukire.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Chenjerani tsono! “Mbale wako akachimwa, umdzudzule. Akatembenuka mtima, umkhululukire.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Nʼchifukwa chake dziyangʼanireni nokha. “Ngati mʼbale wanu achimwa, mudzudzuleni, ndipo ngati alapa, mukhululukireni.

Onani mutuwo Koperani




Luka 17:3
18 Mawu Ofanana  

Akandipanda munthu wolungama ndidzati nchifundo: akandidzudzula, ndidzakuyesa mafuta a pamutu; mutu wanga usakane: Pakuti pangakhale posautsidwa iwo ndidzawapempherera.


Dzichenjere ungachite pangano ndi anthu a ku dziko limene umukako, lingakhale msampha pakati panu;


Chidzudzulo chilowa m'kati mwa wozindikira, kopambana ndi kukwapula wopusa kwambiri.


Chidzudzulo chomveka chiposa chikondi chobisika.


Usadzudzule wonyoza kuti angakude; dzudzula wanzeru adzakukonda.


Usamamuda mbale wako mumtima mwako; umdzudzule munthu mnzako ndithu, usadzitengera uchimo chifukwa cha iye.


Pamenepo Petro anadza, nati kwa Iye, Ambuye, mbale wanga adzandilakwira kangati, ndipo ine ndidzamkhululukira iye? Kufikira kasanu ndi kawiri kodi?


Koma mudziyang'anire nokha, kuti kapena mitima yanu ingalemetsedwe ndi madyaidya ndi kuledzera, ndi zosamalira za moyo uno, ndi kuti tsiku ilo lingafikire inu modzidzimutsa ngati msampha;


Potero, penyani bwino umo muyendera, si monga opanda nzeru, koma monga anzeru;


Potero dzichenjerani nao moyo wanu ndithu; popeza simunapenye mafanidwe konse tsikuli Yehova ananena ndi inu mu Horebu, ali pakati pa moto;


Dzichenjerani, mungaiwale chipangano cha Yehova Mulungu wanu, chimene anapangana nanu, ndi kuti mungadzipangire fano losema, chifaniziro cha kanthu kalikonse Yehova Mulungu wanu anakuletsani.


Chokhachi, dzichenjerani nokha, ndi kusunga moyo wanu mwachangu, kuti mungaiwale zinthuzi adaziona maso anu, ndi kuti zisachoke kumtima kwanu masiku onse a moyo wanu; koma muzidziwitsa ana anu ndi zidzukulu zanu.


ndi kuyang'anira kuti pangakhale wina wakuperewera chisomo cha Mulungu, kuti ungapuke muzu wina wa kuwawa mtima ungavute inu, ndipo aunyinji angadetsedwe nao;


Abale anga, ngati wina wa inu asochera posiyana ndi choonadi, ndipo ambweza iye mnzake;


Mudzipenyerere nokha, kuti mungataye zimene tazichita, koma kuti mulandire mphotho yokwanira.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa