Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 16:21 - Buku Lopatulika

21 ndipo anafuna kukhuta ndi zakugwa pa gome la mwini chumayo; komatu agalunso anadza nanyambita zilonda zake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

21 ndipo anafuna kukhuta ndi zakugwa pa gome la mwini chumayo; komatu agalunso anadza nanyambita zilonda zake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

21 Ankalakalaka kudya nyenyeswa zimene zinkagwa pansi kuchokera pa tebulo la wachuma uja. Koma si pokhapo, ngakhale agalu ankabwera kumadzanyambita zilonda zake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

21 ndipo ankafunitsitsa atadya zomwe zinkagwa pansi kuchokera pamene munthu wolemerayo amadyerapo. Agalu ankabweranso ndi kumanyambita zilonda zake.

Onani mutuwo Koperani




Luka 16:21
7 Mawu Ofanana  

Koma iye anati, Eetu, Ambuye, pakutinso tiagalu timadya nyenyeswa zakugwa pagome pa ambuye ao.


Koma iye anavomera nanena ndi Iye, Inde Ambuye; tingakhale tiagalu ta pansi pa gome tikudyako nyenyeswa za ana.


ndipo wopemphapempha wina, dzina lake Lazaro, adaikidwa pakhomo pake wodzala ndi zilonda,


Ndipo kunali kuti wopemphayo adafa, ndi kuti anatengedwa iye ndi angelo kunka kuchifuwa cha Abrahamu; ndipo mwini chumayo adafanso, naikidwa m'manda.


Ndipo pamene adakhuta, Iye ananena kwa ophunzira ake, Sonkhanitsani makombo kuti kasatayike kanthu.


Kufikira nthawi yomwe ino timva njala, timva ludzu, tili amaliseche, tikhomedwa, tilibe pokhazikika;


m'chivutitso ndi m'cholemetsa, m'madikiro kawirikawiri, m'njala ndi ludzu, m'masalo a chakudya kawirikawiri, m'chisanu ndi umaliseche.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa