Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 15:21 - Buku Lopatulika

21 Ndipo mwanayo anati kwa iye, Atate ndinachimwira Kumwamba ndi pamaso panu, sindiyeneranso konse kutchulidwa mwana wanu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

21 Ndipo mwanayo anati kwa iye, Atate ndinachimwira Kumwamba ndi pamaso panu, sindiyeneranso konse kutchulidwa mwana wanu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

21 Mwanayo adati, ‘Atate, ndidachimwira Mulungu wakumwamba, ndi inu nomwe. Sindili woyenera kuchedwanso mwana wanu.’

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

21 “Mwanayo anati, ‘Abambo, ine ndachimwira kumwamba ndi inunso. Ine sindiyenera konse kutchedwa mwana wanu.’

Onani mutuwo Koperani




Luka 15:21
10 Mawu Ofanana  

Apenyerera anthu, ndi kuti, ndinachimwa, ndaipsa choongokacho, ndipo sindinapindule nako.


Ndipo musaitane mlandu wa mtumiki wanu; pakuti pamaso panu sipadzakhala wolungama wamoyo mmodzi yense.


Pa Inu, Inu nokha, ndinachimwa, ndipo ndinachichita choipacho pamaso panu; kuti mukhale wolungama pakulankhula Inu, mukhalenso woyera pa kuweruza kwanu.


Koma vomereza zoipa zako, kuti walakwira Yehova Mulungu wako, ndi kupatukira mwa alendo patsinde pa mitengo yaiwisi yonse, ndipo sunamvere mau anga, ati Yehova.


kuti uzikumbukira ndi kuchita manyazi ndi kusatsegulanso pakamwa pako konse, chifukwa chamanyazi ako, pamene ndikufafanizira zonse unazichita, ati Ambuye Yehova.


Ndipo iye ananyamuka, nadza kwa atate wake. Koma pakudza iye kutali atate wake anamuona, nagwidwa chifundo, nathamanga, namkupatira pakhosi pake, nampsompsonetsa.


Koma atateyo ananena kwa akapolo ake, Tulutsani msanga mwinjiro wokometsetsa, nimumveke; ndipo mpatseni mphete kudzanja lake ndi nsapato kumapazi ake;


Kapena upeputsa kodi kulemera kwa ubwino wake, ndi chilekerero ndi chipiriro chake, wosadziwa kuti ubwino wa Mulungu ukubwezera kuti ulape?


Koma pakuchimwira abale, ndi kulasa chikumbumtima chao chofooka, muchimwira kotero Khristu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa