Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 11:40 - Buku Lopatulika

40 Opusa inu, kodi Iye wopanga kunja kwake sanapangenso m'kati mwake?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

40 Opusa inu, kodi Iye wopanga kunja kwake sanapangenso m'kati mwake?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

40 Ndinu anthu opusa! Kodi Mulungu amene adapanga zakunja, si yemweyo adapanganso zam'kati?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

40 Anthu opusa inu! Kodi amene anapanga zamʼkati sanapangenso zakunja?

Onani mutuwo Koperani




Luka 11:40
17 Mawu Ofanana  

Ndipo anati Mulungu, Tipange munthu m'chifanizo chathu, monga mwa chikhalidwe chathu: alamulire pansomba za m'nyanja, ndi pambalame za m'mlengalenga, ndi pang'ombe, ndi padziko lonse lapansi, ndi pazokwawa zonse zakukwawa padziko lapansi.


Ndipo Yehova Mulungu anaumba munthu ndi dothi lapansi, nauzira mpweya wa moyo m'mphuno mwake; munthuyo nakhala wamoyo.


Wauchitsiru amati mumtima mwake, Kulibe Mulungu. Achita zovunda, achita ntchito zonyansa; kulibe wakuchita bwino.


Iye amene akonza mitima ya iwo onse, amene azindikira zochita zao zonse.


Kodi mudzakonda zazibwana kufikira liti, achibwana inu? Onyoza ndi kukonda kunyoza, opusa ndi kuda nzeru?


Achibwana inu, chenjerani, opusa inu, khalani ndi mtima wozindikira;


Tamvanitu ichi, inu anthu opusa, ndi opanda nzeru; ali ndi maso koma osaona, ali ndi makutu koma osamva;


Katundu wa mau a Yehova wakunena Israele. Atero Yehova, wakuyala miyamba, ndi kuika maziko a dziko lapansi, ndi kulenga mzimu wa munthu m'kati mwake;


Ndipo anagwa nkhope zao pansi, nati, Mulungu, ndinu Mulungu wa mizimu ya anthu onse, walakwa munthu mmodzi, ndipo kodi mukwiya nalo khamu lonse?


Inu opusa, ndi akhungu: pakuti choposa nchiti, golide kodi, kapena Kachisi amene ayeretsa golideyo?


Mfarisi iwe wakhungu, yambawatsuka m'kati mwa chikho ndi mbale, kuti kunja kwake kukhalenso koyera.


Koma Mulungu anati kwa iye, Wopusa iwe, usiku womwe uno udzafunidwa moyo wako; ndipo zinthu zimene unazikonza zidzakhala za yani?


Ndipo Iye anati kwa iwo, Opusa inu, ndi ozengereza mtima kusakhulupirira zonse adazilankhula aneneri!


Wopusa iwe, chimene uchifesa wekha sichikhalitsidwanso chamoyo, ngati sichifa;


Komanso, tinali nao atate a thupi lathu akutilanga, ndipo tinawalemekeza; kodi sitidzagonjera Atate wa mizimu koposa nanga, ndi kukhala ndi moyo?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa