Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Levitiko 4:11 - Buku Lopatulika

11 Natulutse chikopa cha ng'ombeyo, ndi nyama yake yonse, pamodzi ndi mutu wake, ndi miyendo yake, ndi matumbo ake, ndi chipwidza chake,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Natulutse chikopa cha ng'ombeyo, ndi nyama yake yonse, pamodzi ndi mutu wake, ndi miyendo yake, ndi matumbo ake, ndi chipwidza chake,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Koma chikopa cha ng'ombe yamphongoyo, pamodzi ndi mnofu wake, mutu wake, miyendo yake, matumbo ake ndi ndoŵe yake,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Koma chikopa cha ngʼombe yayimunayo ndi mnofu wake wonse, pamodzi ndi mutu ndi miyendo, zamʼkati ndi matumbo,

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 4:11
11 Mawu Ofanana  

Monga kum'mawa kutanimpha ndi kumadzulo, momwemo anatisiyanitsira kutali zolakwa zathu.


Koma nyama ya ng'ombeyo, ndi chikopa chake, ndi chipwidza chake, uzitentha izi ndi moto kunja kwa chigono; ndiyo nsembe yauchimo.


Koma ng'ombe ya nsembe yauchimo, ndi mbuzi ya nsembe yauchimo, zimene mwazi wao analowa nao kuchita nao chotetezera m'malo opatulika, atuluke nazo kunja kwa chigono; natenthe ndi moto zikopa zao, ndi nyama zao, ndi chipwidza chao.


umo azikachotsera pa ng'ombe ya nsembe yoyamika; ndipo wansembe azitenthe paguwa la nsembe yopsereza.


Ndipo atulutse ng'ombeyo kunja kwa chigono, ndi kuitentha monga anatenthera ng'ombe yoyamba ija; ndiyo nsembe yauchimo ya kwa msonkhano.


Koma asadye nsembe yauchimo iliyonse, imene amadza nao mwazi wake ku chihema chokomanako kutetezera nao m'malo opatulika; aitenthe ndi moto.


ndipo muipereke kwa Eleazara wansembe, naitulutse iye kunja kwa chigono, ndipo wina aiphe pamaso pake.


Pamenepo atenthe ng'ombe yaikaziyo pamaso pake; atenthe chikopa chake ndi nyama yake, ndi mwazi wake, pamodzi ndi chipwidza chake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa