Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Levitiko 26:5 - Buku Lopatulika

5 Ndipo nyengo yopuntha tirigu idzafikira nyengo yotchera mphesa, ndi nyengo yotchera mphesa idzafikira nyengo zobzala; ndipo mudzakhuta nacho chakudya chanu, ndi kukhala m'dziko mwanu okhazikika.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Ndipo nyengo yopuntha tirigu idzafikira nyengo yotchera mphesa, ndi nyengo yotchera mphesa idzafikira nyengo zobzala; ndipo mudzakhuta nacho chakudya chanu, ndi kukhala m'dziko mwanu okhazikika.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Mudzakhala mukupuntha dzinthu mpaka nthaŵi yothyola zipatso, ndipo mudzakhala mukuthyola zipatso mpaka nthaŵi yobzala. Mudzadya chakudya mpaka kukhuta, ndi kumakhala m'dziko mwanu popanda chokuvutani.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Mudzakhala mukupuntha tirigu mpaka nthawi yothyola mphesa, ndipo mudzakhala mukuthyola mphesa mpaka nthawi yodzala. Mudzadya chakudya chanu mpaka kukhuta ndipo mudzakhala mʼdziko lanu mwamtendere.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 26:5
26 Mawu Ofanana  

Kuti nkhokwe zathu zidzale, kutipatsa za mitundumitundu; ndi kuti nkhosa zathu ziswane zikwizikwi, inde zikwi khumi kubusako.


Ambuye, Inu munatikhalira mokhalamo m'mibadwomibadwo.


Nanenanso Mose, Pakukupatsani Yehova nyama ya kudya madzulo, ndi mkate wokhuta m'mawa, atero popeza Yehova adamva madandaulo anu amene mumdandaulira nao. Koma ife ndife chiyani? Simulikudandaulira ife koma Yehova.


Koma wondimvera ine adzakhala osatekeseka, nadzakhala phee osaopa zoipa.


Dzina la Yehova ndilo nsanja yolimba; wolungama athamangiramo napulumuka.


Ngati inu muli ofuna ndi omvera, mudzadya zabwino za dziko,


Ndipo Mulungu adzapatsa mvula ya mbeu yako, ukaibzale m'nthaka; ndi mkate ndiwo phindu la nthaka, ndipo tirigu wake adzacha bwino ndi kuchuluka; tsiku limenelo ng'ombe zako zidzadya m'madambo aakulu.


Masiku ake Yuda adzapulumutsidwa, ndipo Israele adzakhala mokhazikika, dzina lake adzatchedwa nalo, ndilo Yehova ndiye chilungamo chathu.


Ndipo tsiku lomwelo ndidzawachitira pangano ndi nyama zakuthengo, ndi mbalame za mlengalenga, ndi zokwawa pansi; ndipo ndidzathyola uta, ndi lupanga, ndi nkhondo, zichoke m'dziko, ndi kuwagonetsa pansi mosatekeseka.


Ndidzakutomeranso ukhale wanga mokhulupirika, ndipo udzadziwa Yehova.


Ndipo Yehova anayankha, nati kwa anthu ake, Taonani, ndidzakutumizirani tirigu, ndi vinyo, ndi mafuta; ndipo mudzakhuta ndi izo; ndipo sindidzakuperekaninso mukhale chitonzo mwa amitundu;


Musamaopa, nyama zakuthengo inu; pakuti m'chipululu muphukanso msipu; pakuti mitengo ibala zipatso zao; mikuyu ndi mipesa ipatsa mphamvu zao.


Ndipo mudzadyaidya ndi kukhuta, nimudzalemekeza dzina la Yehova Mulungu wanu, amene anachita nanu modabwitsa; ndi anthu anga sadzachita manyazi nthawi zonse.


Taonani, akudza masiku, ati Yehova, akuti wolima adzapezana ndi wodula, ndi woponda mphesa adzapezana ndi wofetsa, ndi mapiri adzakhetsa vinyo watsopano, ndi zitunda zonse zidzasungunuka.


Ha, Yerusalemu, Yerusalemu, amene umapha aneneri, ndi kuwaponya miyala iwo otumidwa kwa iwe! Ine ndinafuna kangati kusonkhanitsa pamodzi ana ako, inde monga thadzi lisonkhanitsa anapiye ake m'mapiko ake, koma inu simunafune ai!


Koma sanadzisiyire Iye mwini wopanda umboni, popeza anachita zabwino, nakupatsani inu zochokera kumwamba mvula ndi nyengo za zipatso, ndi kudzaza mitima yanu ndi chakudya ndi chikondwero.


Ndipo ndidzapatsa msipu wa zoweta zanu podyetsa panu; mudzadyanso nimudzakhuta.


Lamulira iwo achuma m'nthawi ino ya pansi pano, kuti asadzikuze, kapena asayembekezere chuma chosadziwika kukhala kwake, koma Mulungu, amene atipatsa ife zonse kochulukira, kuti tikondwere nazo;


amene musungidwa ndi mphamvu ya Mulungu mwa chikhulupiriro, kufikira chipulumutso chokonzeka kukavumbulutsidwa nthawi yotsiriza.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa