Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Levitiko 20:2 - Buku Lopatulika

2 Unenenso kwa ana a Israele ndi kuti, Aliyense wa ana a Israele, kapena wa alendo akukhala mu Israele, amene apereka mbeu zake kwa Moleki, azimupha ndithu; anthu a m'dziko amponye miyala.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Unenenso kwa ana a Israele ndi kuti, Aliyense wa ana a Israele, kapena wa alendo akukhala m'Israele, amene apereka mbeu zake kwa Moleki, azimupha ndithu; anthu a m'dziko amponye miyala.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 “Uza Aisraele kuti: Mwisraele aliyense, kapena mlendo wokhala nao m'dziko mwanu, akapereka ana ake kwa Moleki, aphedwe: anthu am'dzikomo amponye miyala.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 “Uza Aisraeli kuti, ‘Mwisraeli aliyense kapena mlendo aliyense wokhala mu Israeli wopereka mwana wake kwa Moleki ayenera kuphedwa. Anthu a mʼdera lakelo amuphe ndi miyala.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 20:2
33 Mawu Ofanana  

Pamenepo Solomoni anamangira Kemosi fano lonyansitsa la Amowabu ndi Moleki fano lonyansitsa la ana a Amoni misanje, paphiri lili patsogolo pa Yerusalemu.


Napititsa ana ao aamuna ndi aakazi kumoto, naombeza ula, nachita zanyanga, nadzigulitsa kuchita choipa pamaso pa Yehova, kuutsa mkwiyo wake.


Anawaipitsiranso Tofeti, wokhala m'chigwa cha ana a Hinomu; kuti asapitirize mmodzi yense mwana wake wamwamuna kapena wamkazi pamoto kwa Moleki.


Nafukizanso yekha m'chigwa cha mwana wa Hinomu, napsereza ana ake m'moto, monga mwa zonyansa za amitundu, amene Yehova anawainga pamaso pa ana a Israele.


Anapititsanso ana ake pamoto m'chigwa cha ana a Hinomu, naombeza maula, nasamalira malodza, nachita zanyanga, naika obwebweta ndi openduza; anachita zoipa zambiri pamaso pa Yehova kuutsa mkwiyo wake.


nakhetsa mwazi wosachimwa, ndiwo mwazi wa ana ao aamuna ndi aakazi, amene anawaperekera nsembe mafano a Kanani; m'mwemo analidetsa dziko ndi mwaziwo.


Ndipo anamanga misanje ya Baala, ili m'chigwa cha mwana wake wa Hinomu, kuti apitirize kumoto ana ao aamuna ndi aakazi chifukwa cha Moleki; chimene sindinawauze, chimene sichinalowe m'mtima mwanga, kuti achite chonyansa ichi, chochimwitsa Yuda.


Namanga akachisi a ku Tofeti, kuli m'chigwa cha mwana wa Hinomu, kuti atenthe m'moto ana ao aamuna ndi aakazi; chimene sindiwanauze iwo, sichinalowe m'mtima mwanga.


ndinawadetsanso m'zopereka zao; pakuti anapititsa pamoto onse oyamba kubadwa kuti ndiwapasule; kuti adziwe kuti Ine ndine Yehova.


Ndipo popereka zopereka zanu popititsa ana anu pamoto, mudzidetsa kodi ndi mafano anu onse mpaka lero lino? Ndipo kodi ndidzafunsidwa ndi inu, nyumba ya Israele? Pali Ine, ati Ambuye Yehova, sindidzafunsidwa ndi inu;


Pakuti anachita chigololo, ndi m'manja mwao muli mwazi, ndipo anachita chigololo ndi mafano ao, nawapititsiranso pamoto ana ao aamuna amene anandibalira, kuti athedwe.


pakuti ataphera mafano ao, ana ao analowa tsiku lomwelo m'malo anga opatulika kuwadetsa; ndipo taona, anatero m'kati mwa nyumba yanga.


Ndipo munthu aliyense wa ana a Israele, kapena mlendo wakugonera pakati pa inu, akasaka nyama kapena mbalame yakudya, nakaigwira; azikhetsa mwazi wake, naufotsere ndi dothi.


Ndipo aliyense wakudya yakufa yokha, kapena yojiwa kuthengo, ngakhale ndiye wa m'dziko kapena mlendo, azitsuka nsalu zake, nasambe ndi madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo; pamenepo adzakhala woyera.


Ndipo uzinena nao, Munthu aliyense wa mbumba ya Israele, kapena mlendo wakugonera pakati panu, amene apereka nsembe yopsereza kapena nsembe yophera,


Ndipo usamapereka a mbumba yako kuwapitiriza kumoto chifukwa cha Moleki; usamaipsa dzina la Mulungu wako; Ine ndine Yehova.


Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,


Munthu wamwamuna kapena wamkazi wakubwebweta, kapena wanyanga, azimupha ndithu; aziwaponya miyala; mwazi wao ukhale pamutu pao.


Tuluka naye wotembererayo kunja kwa chigono; ndipo onse adamumva aike manja ao pamutu pake, ndi khamu lonse limponye miyala afe.


Ndi iye wakuchitira mwano dzina la Yehova, amuphe ndithu; khamu lonse limponye miyala ndithu; mlendo ndi wobadwa m'dziko yemwe akachitira dzina la Yehova mwano, awaphe.


Ndipo Mose ananena ndi ana a Israele, ndipo anatulutsa wotembererayo kunja kwa chigono, namponya miyala. Ndipo ana a Israele anachita monga Yehova adauza Mose.


Ndipo munatenga chihema cha Moleki, ndi nyenyezi ya mulungu Refani, zithunzizo mudazipanga kuzilambira; ndipo ndidzakutengani kunka nanu m'tsogolo mwake mwa Babiloni.


Musamatero ndi Yehova Mulungu wanu; pakuti zilizonse zinyansira Yehova, zimene azida Iye, iwowa anazichitira milungu yao; pakuti angakhale ana ao aamuna ndi ana ao aakazi awatentha m'moto, nsembe ya milungu yao.


Akapeza pakati panu, m'mudzi wanu wina umene anakupatsani Yehova Mulungu wanu, wamwamuna kapena wamkazi wakuchita chili choipa pamaso pa Yehova Mulungu wanu, ndi kulakwira chipangano chake,


Asapezeke mwa inu munthu wakupitiriza mwana wake wamwamuna kapena mwana wake wamkazi ku moto wa ula, wosamalira mitambo, kapena wosamalira kulira kwa mbalame, kapena wanyanga.


Pamenepo amuna onse a mzinda wake amponye miyala kuti afe; chotero muchotse choipacho pakati panu; ndipo Israele wonse adzamva, nadzaopa.


pamenepo azimtulutsa namwaliyo ku khomo la nyumba ya atate wake, ndipo amuna a mzinda wake azimponya miyala kuti afe; popeza anachita chopusa mu Israele, kuchita chigololo m'nyumba ya atate wake; chotero uzichotsa choipacho pakati panu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa