Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Levitiko 17:9 - Buku Lopatulika

9 osadza nayo ku khomo la chihema chokomanako, kuiphera Yehova; amsadze munthuyu kumchotsa kwa anthu a mtundu wake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 osadza nayo ku khomo la chihema chokomanako, kuiphera Yehova; amsadze munthuyu kumchotsa kwa anthu a mtundu wake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 akapanda kubwera nayo pakhomo pa chihema chamsonkhano kudzaipereka pamaso pa Chauta, munthu ameneyo achotsedwe pakati pa anthu anzake.’

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 popanda kubwera nayo pa khomo la tenti ya msonkhano kudzayipereka pamaso pa Yehova, munthu ameneyo achotsedwe pakati pa anthu anzake.’ ”

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 17:9
6 Mawu Ofanana  

Undiumbire guwa la nsembe ladothi, nundiphere pomwepo nsembe zako zopsereza, ndi nsembe zako zamtendere, nkhosa zako ndi ng'ombe zako; paliponse ndikumbukiritsa anthu dzina langa ndidzakudzera ndi kukudalitsa.


Aliyense amene akonza ena otere, kapena aliyense awaika pa mlendo, ameneyo asazidwe kwa anthu a mtundu wake.


Chopereka chake chikakhala nsembe yopsereza ya ng'ombe, azibwera nayo yaimuna yopanda chilema; abwere nayo ku khomo la chihema chokomanako, kuti alandirike pamaso pa Yehova.


osadza nayo ku khomo la chihema chokomanako, kuti aipereke chopereka cha Yehova, ku bwalo la Kachisi wa Yehova; azimuyesa munthuyu wochimwira mwazi, wakhetsa mwazi; ndipo amsadze munthuyo kumchotsa pakati pa anthu a mtundu wake;


Ndipo uzinena nao, Munthu aliyense wa mbumba ya Israele, kapena mlendo wakugonera pakati panu, amene apereka nsembe yopsereza kapena nsembe yophera,


akabwera nayo nkhosa kuti ikhale chopereka chake, abwere nayo pamaso pa Yehova;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa