Hoseya 1:10 - Buku Lopatulika10 Angakhale anatero, kuwerenga kwake kwa ana a Israele kudzanga mchenga wa kunyanja, wosayeseka kapena kuwerengeka; ndipo kudzatero kuti m'mene adawanena, Simuli anthu anga, adzanena nao, Muli ana a Mulungu wamoyo. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201410 Angakhale anatero, kuwerenga kwake kwa ana a Israele kudzanga mchenga wa kunyanja, wosayeseka kapena kuwerengeka; ndipo kudzatero kuti m'mene adawanena, Simuli anthu anga, adzanena nao, Muli ana a Mulungu wamoyo. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa10 Komabe Aisraele adzachuluka ngati mchenga wakunyanja umene sangathe kuuyesa kapena kuuŵerenga. Pamalo pamene Mulungu adaanena anthuwo kuti “Sindinu anthu anga,” pomweponso adzaŵatchula kuti, “Ana a Mulungu Wamoyo.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero10 “Komabe Aisraeli adzachuluka ngati mchenga wa mʼmbali mwa nyanja umene sangathe kuwuyeza kapena kuwuwerenga. Pamalo omwe ananena kuti, ‘Sindinu anthu anga,’ pomweponso adzawatchula kuti ‘Ana a Mulungu wamoyo.’ Onani mutuwo |
Ndipo iwo adzatenga abale anu onse mwa amitundu onse akhale nsembe ya kwa Yehova; adzabwera nao pa akavalo, ndi m'magaleta, ndi m'machila, ndi pa nyuru, ndi pa ngamira, kudza kuphiri langa lopatulika ku Yerusalemu, ati Yehova, monga ana a Israele abwera nazo nsembe zao m'chotengera chokonzeka kunyumba ya Yehova.