Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 48:10 - Buku Lopatulika

10 Koma maso a Israele anali akhungu mu ukalamba wake, ndipo sanathei kuona. Ndipo anadza nao pafupi; ndipo anapsompsona iwo, nawafungatira.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Koma maso a Israele anali akhungu m'ukalamba wake, ndipo sanathei kuona. Ndipo anadza nao pafupi; ndipo anapsompsona iwo, nawafungatira.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Maso a Yakobe sankapenya bwino chifukwa cha ukalamba. Yosefe adabwera nawo kwa iye anawo ndipo Yakobe adaŵakumbatira, naŵampsompsona.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Koma maso a Israeli anali ofowoka chifukwa cha kukalamba moti sankaona nʼkomwe. Tsono Yosefe anabwera nawo ana ake aja pafupi ndi abambo ake ndipo abambo ake anawapsompsona nawakumbatira.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 48:10
13 Mawu Ofanana  

Ndipo panali atakalamba Isaki, ndi maso ake anali akhungu losaona nalo, anamuitana Esau mwana wake wamwamuna wamkulu, nati kwa iye, Mwana wanga; ndipo anati kwa iye, Ndine pano.


Ndipo anasendera nampsompsona; ndipo anamva kununkhira kwa zovala zake, namdalitsa, nati, Taona, kununkhira kwa mwana wanga, kufanana ndi kununkhira kwa munda anaudalitsa Yehova;


M'mamawa Labani anauka nampsompsona ana ake aamuna ndi aakazi, nawadalitsa: ndipo Labani anachoka, nabwera kumalo kwake.


Ndipo anampsompsona abale ake onse, nalirira iwo; ndipo pambuyo pake abale ake onse anacheza naye.


Ndipo Israele anati kwa Yosefe, Sindinaganizira kuti ndiona nkhope yako: ndipo, taona, Mulungu wandionetsa ine mbeu zako zomwe.


Ndipo Israele anayang'ana ana aamuna a Yosefe, nati, Ndani awa?


Ndipo iye anasiya ng'ombe zija, namthamangira Eliya, nati, Ndiloleni ndiyambe ndakampsompsona atate wanga ndi amai wanga; nditatero ndidzakutsatani. Nati iye, Bwerera ndakuchitanji?


tsikulo omwe asunga nyumba adzanthunthumira, amuna olimba nadzawerama, akupera nadzaleka poperewera, omwe ayang'ana pamazenera nadzadetsedwa;


Taonani, mkono wa Yehova sufupika, kuti sungathe kupulumutsa; khutu lake silili logontha, kuti silingamve;


Nenepetsa mtima wa anthu awa, lemeretsa makutu ao, nutseke maso ao; angaone ndi maso ao, angamve ndi makutu ao, angazindikire ndi mtima wao, nakabwerenso, nachiritsidwe.


Ndipo zaka zake za Mose ndizo zana limodzi ndi makumi awiri, pakumwalira iye; diso lake silinachite mdima, ndi mphamvu yake siidaleke.


Ndipo kunali nthawi yomweyo Eli atagona m'malo mwake (maso ake anayamba chizirezire osatha kupenya bwino);


Koma Eli anali ndi zaka makumi asanu ndi anai kudza zisanu ndi zitatu; ndipo maso ake anangokhala tong'o osapenya.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa