Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 47:23 - Buku Lopatulika

23 Ndipo Yosefe anati kwa anthu, Taonani, ndamgulira Farao inu ndi dziko lanu lero lomwe, taonani, mbeu zanu siizi, mubzale m'dziko.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

23 Ndipo Yosefe anati kwa anthu, Taonani, ndamgulira Farao inu ndi dziko lanu lero lomwe, taonani, mbeu zanu siizi, mubzale m'dziko.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

23 Yosefe adauza anthu kuti, “Onani tsopano ndakugulani pamodzi ndi minda yanu yonse, kugulira Farao. Tsono nazi mbeu, mubzale m'minda mwanu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

23 Yosefe anati kwa anthuwo, “Tsono poti ndakugulani inu ndi minda yanu, kugulira Farao. Nayi mbewu kuti mudzale mʼminda yanu.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 47:23
15 Mawu Ofanana  

Ng'ombe zazikazi zisanu ndi ziwiri zoonda ndi za maonekedwe oipa zinatuluka pambuyo pao ndizo zaka zisanu ndi ziwiri, ndiponso ngala zisanu ndi ziwiri zopanda kanthu zopserera ndi mphepo ya kum'mawa, ndizo zaka zisanu ndi ziwiri za njala.


Zaka ziwirizi muli njala m'dziko muno; ndipo zatsala zaka zisanu, zopanda kulima kapena kusenga.


Koma dziko la ansembe lokha sanagule, chifukwa ansembe analandira gawo lao kwa Farao, nadya gawolo anawapatsa Farao; chifukwa chake sanagulitse dziko lao.


Ndipo padzakhala pakukunkha, muzipatsa limodzi la mwa magawo asanu kwa Farao, koma magawo anai ndi anu, mbeu za munda, ndi za chakudya chanu, ndi cha ana anu ndi mabanja anu.


Wodala munthu wakuchitira chifundo, nakongoletsa; adzalimbika nao mlandu wake poweruzidwa.


Wodala iye amene asamalira wosauka! Tsiku la tsoka Yehova adzampulumutsa.


Womana tirigu anthu amtemberera; koma madalitso adzakhala pamutu pa wogulitsa.


Zakudya zikwanira wolima minda yake; koma wotsata anthu opanda pake asowa nzeru.


M'kulima kwa osauka muli zakudya zambiri; koma zinazo zimaonongeka posowa chiweruzo.


Mamawa fesa mbeu zako, madzulonso osapumitsa dzanja lako; pakuti sudziwa ziti zidzalola bwino ngakhale izizi, ngakhale izozo, kaya zonse ziwiri zidzakhala bwino.


Pakuti monga mvula imagwa pansi ndi matalala, kuchokera kumwamba yosabwerera komweko, koma ikhamiza nthaka ndi kuibalitsa, ndi kuiphukitsa, ndi kuipatsitsa mbeu kwa wobzala, ndi chakudya kwa wakudya;


Ndani kodi ali kapolo wokhulupirika ndi wanzeru, amene mbuye wake anamkhazika woyang'anira banja lake, kuwapatsa zakudya pa nthawi yake?


Ndipo iye wopatsa mbeu kwa wofesa, ndi mkate ukhale chakudya, adzapatsa ndi kuchulukitsa mbeu yanu yofesa, nadzaonjezapo pa zipatso za chilungamo chanu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa