Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 3:14 - Buku Lopatulika

14 Ndipo anati Yehova Mulungu kwa njokayo, Chifukwa kuti wachita ichi, wotembereredwa ndiwe wopambana ndi zinyama zonse ndi zamoyo zonse za m'thengo: uziyenda ndi pamimba pako, uzidya fumbi masiku onse a moyo wako:

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Ndipo anati Yehova Mulungu kwa njokayo, Chifukwa kuti wachita ichi, wotembereredwa ndiwe wopambana ndi zinyama zonse ndi zamoyo zonse za m'thengo: uziyenda ndi pamimba pako, uzidya fumbi masiku onse a moyo wako:

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Pamenepo Chauta adauza njokayo kuti, “Chifukwa chakuti wachita zimenezi, ndiwe wotembereredwa pakati pa nyama zonse za pansi pano, zoŵeta ndi zakuthengo zomwe. Kuyambira tsopano mpaka muyaya udzakwaŵa ndi kumimba kwako, ndipo chakudya chako chidzakhala fumbi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Choncho Yehova Mulungu anati kwa njokayo, “Popeza wachita zimenezi, “Ndiwe wotembereredwa kuposa ziweto zonse ndi nyama zakuthengo zonse. Udzayenda chafufumimba ndipo udzadya fumbi masiku onse a moyo wako.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 3:14
10 Mawu Ofanana  

Ndipo njoka inali yochenjera yoposa zamoyo zonse za m'thengo zimene anazipanga Yehova Mulungu. Ndipo inati kwa mkaziyo, Eya! Kodi anatitu Mulungu, Usadye mitengo yonse ya m'mundamu?


Tsopano ndiwe wotembereredwa kunthaka, imene inatsegula pakamwa pake kulandira padzanja lako mwazi wa mphwako:


Amene akhetsa mwazi wa munthu, ndi munthunso mwazi wake udzakhetsedwa: chifukwa m'chifanizo cha Mulungu Iye anampanga munthu.


Okhala m'chipululu adzagwadira pamaso pake; ndi adani ake adzaluma nthaka.


Ndipo iwe udzagwetsedwa pansi, nudzanena uli pansi, ndi kulankhula kwako kudzakhala pansi kotuluka m'fumbi; ndi mau ako adzakhala ngati a wina amene ali ndi mzimu wobwebweta, kuchokera pansi, ndi kulankhula kwako kudzakhala konong'ona kochokera m'fumbi.


Mmbulu ndi mwanawankhosa zidzadyera pamodzi; ndi mkango udzadya udzu ngati ng'ombe; ndi fumbi lidzakhala chakudya cha njoka; sizidzapwetekana, kapena kusakazana m'phiri langa lonse lopatulika, ati Yehova.


Potero musiyanitse pakati pa nyama zoyera ndi nyama zodetsa, ndi pakati pa mbalame zodetsa ndi zoyera; ndipo musadzinyansitsa ndi nyama, kapena mbalame, kapena ndi kanthu kalikonse kakukwawa pansi, kamene ndinakusiyanitsirani kakhale kodetsa.


Adzanyambita fumbi ngati njoka; ngati zokwawa za padziko, adzanjenjemera potuluka m'ngaka mwao; adzafika kwa Yehova Mulungu wao ndi mantha, nadzaopa chifukwa cha iwe.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa