Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 28:18 - Buku Lopatulika

18 Yakobo ndipo anauka m'mamawa, natenga mwala umene anaika pansi pamutu wake, nauimiritsa, nathira mafuta pamutu pake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 Yakobo ndipo anauka m'mamawa, natenga mwala umene anaika pansi pa mutu wake, nauimiritsa, nathira mafuta pamtu pake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 Yakobeyo adadzuka m'maŵa kwambiri, natenga mwala uja adaatsamirawu, nauimiritsa kuti ukhale mwala wachikumbutso. Tsono adauthira mafuta mwalawo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 Mmamawa mwake Yakobo anatenga mwala umene anatsamira mutu wake uja nawuyimika ngati chipilala ndi kuthira mafuta pamwamba pake

Onani mutuwo Koperani




Genesis 28:18
16 Mawu Ofanana  

Ndipo Abrahamu analawira m'mamawa, natenga mkate ndi thumba la madzi, nampatsa Hagara, naika paphewa pake, ndi mwana, namchotsa iye: ndipo iye anamuka, nasocherera m'chipululu cha Beereseba.


Ndipo Abrahamu analawira m'mamawa namanga bulu wake, natengako anyamata ake awiri pamodzi naye, ndi Isaki mwana wake, nawaza nkhuni za nsembe yopsereza, nauka, nanka kumalo komwe Mulungu anamuuza iye.


Ndipo anafika kumalo, nagona kumeneko usiku, chifukwa lidalowa dzuwa: ndipo anatenga mwala wa kumeneko, nauika pansi pamutu wake, nagona tulo kumeneko.


Ine ndine Mulungu wa ku Betele, kuja unathira mafuta pamwala paja, pamene unandilumbirira ine chilumbiriro: tsopano uka, nuchoke m'dziko lino, nubwerere ku dziko la abale ako.


Ndipo Yakobo anatenga mwala, nauimiritsa.


Ndipo Yakobo anaimiritsa mwala pamalo pamene ananena ndi iye, choimiritsa chamwala: ndipo anathira pamenepo nsembe yothira, nathirapo mafuta.


Ndipo Yakobo anaimiritsa mwala pamanda pake: umenewo ndi choimiritsa cha pa manda a Rakele kufikira lero.


Koma Abisalomu akali moyo adatenga nadziutsira choimiritsacho chili m'chigwa cha mfumu; pakuti anati, Ndilibe mwana wamwamuna adzakhala chikumbutso cha dzina langa; natcha choimiritsacho ndi dzina la iye yekha; ndipo chitchedwa chikumbutso cha Abisalomu, kufikira lero lomwe.


Ndinafulumira, osachedwa, kusamalira malamulo anu.


Chilichonse dzanja lako lichipeza kuchichita, uchichite ndi mphamvu yako; pakuti mulibe ntchito ngakhale kulingirira ngakhale kudziwa, ngakhale nzeru, kumanda ulikupitako.


Tsiku limenelo padzakhala guwa la nsembe la Yehova pakati padziko la Ejipito, ndi choimiritsa cha Yehova m'malire ake.


Ndipo kunali kuti tsiku lomwe Mose anatsiriza kuutsa chihema, nachidzoza ndi kuchipatula, ndi zipangizo zake zonse, ndi guwa la nsembe, ndi zipangizo zake zonse, nazidzoza ndi kuzipatula;


Ndipo Yoswa anaimika miyala khumi ndi iwiri pakati pa Yordani, poimapo mapazi a ansembe akusenza likasa la chipangano; ikhala komweko kufikira lero lino.


Pamenepo Samuele anatenga mwala nauimika pakati pa Mizipa ndi Sene, nautcha dzina lake Ebenezeri, nati, Kufikira pano Yehova anatithandiza.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa