Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 28:16 - Buku Lopatulika

16 Ndipo Yakobo anauka m'tulo take, nati, Ndithu, Yehova ali mommuno; ndipo sindinadziwe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Ndipo Yakobo anauka m'tulo take, nati, Ndithu, Yehova ali mommuno; ndipo sindinadziwe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Yakobe atadzuka adati, “Ndithudi Chauta ali pano, ndipo ine sindimadziŵa.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Yakobo atadzidzimuka, anati, “Zoonadi Yehova ali pa malo ano, ndipo ine sindinadziwe.”

Onani mutuwo Koperani




Genesis 28:16
14 Mawu Ofanana  

Ndipo Solomoni anauka, ndipo taona, ndilo loto; nabwera ku Yerusalemu, naima ku likasa la chipangano cha Yehova, napereka nsembe zopsereza ndi nsembe zamtendere, nakonzera anyamata ake onse madyerero.


Pakuti Mulungu alankhula kamodzi, kapena kawiri, koma anthu sasamalira.


Taona, Mulungu apita pali ine, koma sindimpenya; napitirira, koma osamzindikira ine.


Ndidzapita kuti kuzembera mzimu wanu? Kapena ndidzathawira kuti kuzembera nkhope yanu?


Inu Mulungu, ndinu woopsa m'malo oyera anu; Mulungu wa Israele ndiye amene apatsa anthu ake mphamvu ndi chilimbiko. Alemekezeke Mulungu.


Afanana ndi Inu ndani mwa milungu, Yehova? Afanana ndi Inu ndani, wolemekezedwa, woyera, woopsa pomyamika, wakuchita zozizwa?


Pamene Yehova anaona kuti adapatuka kukapenya, Mulungu ali m'kati mwa chitsamba, anamuitana, nati, Mose, Mose. Ndipo anati, Ndili pano.


Ndipo Iye anati, Usayandikire kuno; vula nsapato zako ku mapazi ako, pakuti pamalo pamene upondapo iwe, mpopatulika.


Yehova wa makamu, Iye mudzamyeretsa; muope Iye, akuchititseni mantha Iye.


Pamenepo ndinauka, ndinaona; ndipo tulo tanga tinandizunira ine.


Ndipo anati, Tamvani, tsono mau anga; pakakhala mneneri pakati pa inu, Ine Yehova ndidzizindikiritsa kwa iye m'masomphenya, ndinena naye m'kulota.


Ndipo kunali, pokhala Yoswa ku Yeriko, anakweza maso ake, napenya, ndipo taona, panaima munthu pandunji pake ndi lupanga lake losolola m'dzanja lake; namuka Yoswa kuli iye, nati iye, Uvomerezana ndi ife kapena ndi adani athu?


Ndipo kazembe wa ankhondo a Yehova anati kwa Yoswa, Vula nsapato yako pa phazi lako; pakuti malo upondapo mpopatulika. Nachita Yoswa chomwecho.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa