Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 26:8 - Buku Lopatulika

8 Ndipo panali atakhala komwe masiku ambiri, Abimeleki mfumu ya Afilisti, anayang'ana kunja kwa zenera, napenya, taona, Isaki analinkuseka ndi Rebeka mkazi wake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Ndipo panali atakhala komwe masiku ambiri, Abimeleki mfumu ya Afilisti, anayang'ana kunja kwa zenera, napenya, taona, Isaki analinkuseka ndi Rebeka mkazi wake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Isaki atakhala kumeneko kanthaŵi ndithu, Abimeleki mfumu ya Afilisti adasuzumira pa zenera kuyang'ana kunja, naona Isaki atakumbatira Rebeka.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Isake atakhalako kumeneko nthawi yayitali, Abimeleki mfumu ya Afilisti, anasuzumira pa zenera kuyangʼana kunja, ndipo anaona Isake akugwiragwira Rebeka, mkazi wake.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 26:8
8 Mawu Ofanana  

ndipo anthu a kumeneko anamfunsa iye za mkazi wake; ndipo iye anati, Ndiye mlongo wanga: chifukwa kuti anaopa kunena, Mkazi wanga; anati, anthu a kumeneko angandiphe ine chifukwa cha Rebeka; popeza anali wokongola pakumuona.


Ndipo Abimeleki anamuitana Isaki nati, Taona, uyo ndi mkazi wako ndithu: kodi bwanji unati, Ndiye mlongo wanga? Ndipo Isaki anati kwa iye, Chifukwa ndinati, Ndingafe chifukwa cha iye.


Pakuti pa zenera la nyumba yanga ndinapenyera pamwamba pake; ndinaona pakati pa achibwana,


Khalani mokondwa ndi mkazi umkonda masiku onse a moyo wako wachabe, umene Mulungu wakupatsa pansi pano masiku ako onse achabe; pakuti ilo ndi gawo lako la m'moyo ndi m'ntchito zimene uvutika nazo pansi pano.


Wokondedwa wanga akunga mphoyo, pena mwana wa mbawala: Taona, aima patseri pakhoma lathu. Apenyera pazenera, nasuzumira pamade.


Pakuti monga mnyamata akwatira namwali, momwemo ana ako aamuna adzakukwatira iwe; ndi monga mkwati akondwera ndi mkwatibwi, momwemo Mulungu wako adzakondwera nawe.


Anapenyerera ali pazenera, nafuula Make wa Sisera, pa sefa wake, achedweranji galeta wake? Zizengerezeranji njinga za magaleta ake?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa