Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 24:11 - Buku Lopatulika

11 Ndipo anagwaditsa ngamira zake kunja kwa mzinda, ku chitsime cha madzi nthawi yamadzulo, nthawi yotuluka akazi kudzatunga madzi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Ndipo anagwaditsa ngamira zake kunja kwa mudzi, ku chitsime cha madzi nthawi yamadzulo, nthawi yotuluka akazi kudzatunga madzi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Atafika, adazigwaditsa pansi ngamirazo pafupi ndi chitsime, kunja kwa mzinda. Anali madzulo ndithu, nthaŵi imene akazi ankabwera kuchitsimeko kudzatunga madzi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Atafika, anagwaditsa pansi ngamira zija pafupi ndi chitsime chimene chinali kunja kwa mzinda uja. Awa anali madzulo ndithu, nthawi imene amayi amapita kukatunga madzi.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 24:11
10 Mawu Ofanana  

Ndipo ndinafika lero kukasupe, ndipo ndinati, Yehova Mulungu wa mbuyanga Abrahamu, ngati mundiyendetsatu bwino njira yanga m'mene ndinkamo ine;


Ndipo anayang'ana, taonani, chitsime m'dambo, ndipo, taonani, magulu atatu a nkhosa alinkugona kumeneko: pakuti pachitsimepo anamwetsa nkhosa; ndipo mwala wa pakamwa pa chitsime unali waukulu.


Pamene Farao anachimva ichi, anafuna kupha Mose. Koma Mose anathawa pankhope pa Farao, nakhala m'dziko la Midiyani; nakhala pansi pachitsime.


Ndipo wansembe wa Midiyani anali nao ana aakazi asanu ndi awiri, amene anadza kudzatunga madzi; ndipo anadzaza mimwero kuti amwetse gulu la atate wao.


Wolungama asamalira moyo wa choweta chake; koma chifundo cha oipa ndi nkhanza.


Kunali ngati ora lachisanu ndi chimodzi. Kunadza mkazi wotuluka mu Samariya kudzatunga madzi. Yesu ananena naye, Undipatse Ine ndimwe.


Posamveka phokoso la amauta potunga madzi, pomwepo adzafotokozera zolungama anazichita Yehova, zolungama anazichita m'madera ake, mu Israele. Pamenepo anthu a Yehova anatsikira kuzipata.


Pakukwera kumzindako anapeza anthu aakazi alikutuluka kuti akatunge madzi, nanena nao, Mlauliyo alipo kodi?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa