Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 18:28 - Buku Lopatulika

28 kapena akaperewera asanu pa olungama makumi asanuwo; kodi mudzaononga mzinda wonse chifukwa cha kuperewera asanu? Ndipo anati, Ndikapeza makumi anai ndi asanu sindidzauononga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

28 kapena akaperewera asanu pa olungama makumi asanuwo; kodi mudzaononga mudzi wonse chifukwa cha kuperewera asanu? Ndipo anati, Ndikapeza makumi anai ndi asanu sindidzauononga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

28 Nanga pa chiŵerengero cha 50 pakangopereŵera anthu asanu okha, bwanji? Kodi mudzaononga mzindawo popeza kuti asoŵa asanu okha?” Chauta adayankha kuti, “Ndikapeza anthu 45 olungama, sindidzaononga mzindawo.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

28 bwanji anthu olungama atacheperapo ndi asanu pa anthu makumi asanu? Kodi mudzawononga mzinda wonse chifukwa cha asanuwo?” Iye anati, “Nditapezamo anthu 45, sindidzawuwononga.”

Onani mutuwo Koperani




Genesis 18:28
7 Mawu Ofanana  

Ndipo anati Yehova, Ndikapeza mu Sodomu olungama makumi asanu m'kati mwa mzinda, ndidzasiya malo onse chifukwa cha iwo.


Ndipo anayankha Abrahamu nati, Taonanitu, ndadziyesera kunena kwa Ambuye, ine ndine fumbi ndi phulusa:


Ndipo ananenanso kwa Iye nati, Kapena akapezedwa makumi anai m'menemo. Ndipo anati, Sindidzachita chifukwa cha makumi anai.


kuti apemphe zachifundo kwa Mulungu wa Kumwamba pa chinsinsi ichi; kuti Daniele ndi anzake asaonongeke pamodzi ndi eni nzeru ena a ku Babiloni.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa