Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 38:25 - Buku Lopatulika

25 Ndipo siliva wa iwo owerengedwa a khamulo ndiwo matalente zana limodzi, ndi masekeli chikwi chimodzi, kudza mazana asanu ndi awiri, mphambu makumi asanu ndi awiri kudza asanu, kuyesa sekeli wa malo opatulika.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

25 Ndipo siliva wa iwo owerengedwa a khamulo ndiwo matalente zana limodzi, ndi masekeli chikwi chimodzi, kudza mazana asanu ndi awiri, mphambu makumi asanu ndi awiri kudza asanu, kuyesa sekeli wa malo opatulika;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

25 Siliva wochokera kwa mpingo wonse wa anthu, anali wolemera makilogaramu 3,430, potsata miyeso ya ku Nyumba ya Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

25 Siliva wochokera ku gulu lonse la anthu anali wolemerera makilogalamu 3,430, potsata miyeso ya ku malo wopatulika.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 38:25
5 Mawu Ofanana  

Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,


Pamene uwerenga ana a Israele, monga mwa mawerengedwe ao, munthu yense apereke kwa Yehova chiombolo cha pa moyo wake, pa kuwerengedwa iwowa; kuti pasakhale mliri pakati pao, pakuwerengedwa iwowa.


Ndipo uzilandira ndalama za choteteza kwa ana a Israele, ndi kuzipereka pa ntchito ya chihema chokomanako; kuti zikhale chikumbutso cha ana a Israele pamaso pa Yehova, kuchita choteteza cha miyoyo yanu.


Werenga khamu lonse la ana a Israele, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba ya makolo ao ndi kuwerenga maina ao, amuna onse mmodzimmodzi.


Werenga khamu lonse la ana a Israele, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, monga mwa nyumba za makolo ao, onse akutulukira kunkhondo mu Israele.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa