Eksodo 37:17 - Buku Lopatulika17 Ndipo anapanga choikaponyali cha golide woona; mapangidwe ake a choikaponyalicho anachita chosula, tsinde lake ndi thupi lake, zikho zake, mitu yake, ndi maluwa ake zinakhala zochokera m'mwemo; Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201417 Ndipo anapanga choikapo nyali cha golide woona; mapangidwe ake a choikapo nyalicho anachita chosula, tsinde lake ndi thupi lake, zikho zake, mitu yake, ndi maluwa ake zinakhala zochokera m'mwemo; Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa17 Pambuyo pake adapanga choikaponyale cha golide wabwino kwambiri. Tsinde lake ndi thunthu lake zinali zagolide, ndipo zonse zinali zosula ndi nyundo. Zikho zake, ndiye kuti nkhunje ndi maluŵa ake, adazipangira kumodzi ndi choikaponyalecho. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero17 Iwo anapanga choyikapo nyale chagolide wabwino kwambiri. Tsinde lake ndi mphanda zake zinasulidwa ndi nyundo. Zikho zake zokhala ndi mphukira ndi maluwa ake zinapangidwa kumodzi. Onani mutuwo |