Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 32:33 - Buku Lopatulika

33 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Iye amene wandichimwira, ndifafaniza yemweyo kumchotsa m'buku langa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

33 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Iye amene wandichimwira, ndifafaniza yemweyo kumchotsa m'buku langa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

33 Apo Chauta adauza Mose kuti, “Yekhayo amene wandilakwira Ine, ndiye amene ndidzachotse dzina lake m'buku langa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

33 Yehova anamuyankha Mose kuti, “Ndidzafuta mʼbuku aliyense amene wandichimwira.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 32:33
13 Mawu Ofanana  

Afafanizidwe m'buku lamoyo, ndipo asalembedwe pamodzi ndi olungama.


Koma ine ndine wozunzika ndi womva zowawa; chipulumutso chanu, Mulungu, chindikweze pamsanje.


Mwadzudzula amitundu, mwaononga woipayo, mwafafaniza dzina lao kunthawi yonka muyaya.


Ndipo Yehova anati kwa Mose, Lembera ichi m'buku, chikhale chikumbutso, nuchimvetse Yoswa; kuti ndidzafafaniza konse chikumbukiro cha Amaleke pansi pa thambo.


Moyo wochimwawo ndiwo udzafa; mwana sadzasenza mphulupulu za atate wake, ndi atate sadzasenza mphulupulu za mwana; chilungamo cha wolungama chidzamkhalira, ndi choipa cha woipa chidzamkhalira,


Taonani, miyoyo yonse ndi yanga, monga moyo wa atate momwemonso moyo wa mwana, ndiyo yanga; moyo wochimwawo ndiwo udzafa.


Ndi munthu aliyense wakugwira ntchito iliyonse tsiku limenelo, ndidzaononga munthuyo pakati pa anthu a mtundu wake.


Yehova sadzamkhululukira, koma pamenepo mkwiyo wa Yehova ndi nsanje yake zidzamfukira munthuyo; ndipo temberero lonse lolembedwa m'buku ili lidzamkhalira; ndipo Yehova adzafafaniza dzina lake pansi pa thambo.


Inde, ndikupemphaninso, mnzanga wa m'goli woona, muthandize akazi awa amene anakangalika nane pamodzi mu Uthenga Wabwino, pamodzi ndi Klemensinso, ndi otsala aja antchito anzanga, amene maina ao ali m'buku la Moyo.


Ndipo adzachilambira onse akukhala padziko, amene dzina lao silinalembedwe m'buku la moyo la Mwanawankhosa, wophedwa kuyambira makhazikidwe a dziko lapansi.


Ndipo ndinaona akufa, aakulu ndi aang'ono alinkuima kumpando wachifumu; ndipo mabuku anatsegulidwa; ndipo buku lina linatsegulidwa, ndilo la moyo; ndipo akufa anaweruzidwa mwa zolembedwa m'mabuku, monga mwa ntchito zao.


Iye amene apambana adzamveka motero zovala zoyera; ndipo sindidzafafaniza ndithu dzina lake m'buku la moyo, ndipo ndidzamvomereza dzina lake pamaso pa Atate wanga, ndi pamaso pa angelo ake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa