Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 31:14 - Buku Lopatulika

14 Ndipo muzisunga Sabata; popeza ndilo lopatulika la kwa inu; aliyense wakuliipsa aphedwe ndithu; pakuti aliyense wakugwira ntchito m'mwemo, munthu ameneyo achotsedwe mwa anthu a mtundu wake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Ndipo muzisunga Sabata; popeza ndilo lopatulika la kwa inu; aliyense wakuliipsa aphedwe ndithu; pakuti aliyense wakugwira ntchito m'mwemo, munthu ameneyo asadzidwe mwa anthu a mtundu wake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Motero muzisunga tsiku la Sabata, chifukwa ndi loyera kwa inu. Munthu aliyense wosalisunga, aphedwe. Aliyense wogwira ntchito pa tsiku limenelo adzachotsedwe pakati pa anthu anzake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 “Motero muzisunga tsiku la Sabata chifukwa ndi loyera kwa inu. Aliyense amene adetsa tsiku la Sabata ayenera kuphedwa. Aliyense amene agwira ntchito iliyonse pa tsikuli ayenera kuchotsedwa pakati pa anthu anzake.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 31:14
17 Mawu Ofanana  

ndi Sabata lanu lopatulika munawadziwitsa, nimunawalamulira malamulo, ndi malemba, ndi chilamulo, mwa dzanja la Mose mtumiki wanu;


Udzikumbukira tsiku la Sabata, likhale lopatulika.


Aliyense amene akonza ena otere, kapena aliyense awaika pa mlendo, ameneyo asazidwe kwa anthu a mtundu wake.


Aliyense wokonza china chotere kununkhizapo, achotsedwe kwa anthu a mtundu wake.


Agwire ntchito masiku asanu ndi limodzi; koma lachisanu ndi chiwiri ndilo Sabata lakupumula, lopatulika la Yehova; aliyense wogwira ntchito tsiku la Sabata aphedwe ndithu.


popeza ananyoza maweruzo anga, osayenda m'malemba anga, naipsa masabata anga; pakuti mitima yao inatsata mafano ao.


Koma anawo anapandukira Ine, sanayende m'malemba anga, kapena kusunga maweruzo anga kuwachita, amene munthu akawachita adzakhala nao ndi moyo; anaipsa masabata anga; pamenepo ndinati ndidzawatsanulira ukali wanga, kuwakwaniritsira mkwiyo wanga m'chipululu.


popeza sanachite maweruzo anga, koma ananyoza malemba anga, naipsa masabata anga, ndi maso ao anatsata mafano a atate ao.


Ndipo pakakhala mlandu, aimeko kuweruza; auweruze monga mwa maweruzo anga, ndipo azisunga malamulo anga, ndi malemba anga, pazikondwerero zanga zonse zoikika; napatulikitse masabata anga.


Ndipo lizikhala kwa inu lemba losatha; mwezi wachisanu ndi chiwiri, tsiku lakhumi la mweziwo, muzidzichepetsa, osagwira ntchito konse, kapena wa m'dziko, kapena mlendo wakukhala pakati panu;


Ngati munthu alandira mdulidwe tsiku la Sabata, kuti chilamulo cha Mose chingapasulidwe; kodi mundikwiyira Ine, chifukwa ndamchiritsadi munthu tsiku la Sabata?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa