Eksodo 29:41 - Buku Lopatulika41 Ndi mwanawankhosa wina ukonze madzulo; umkonze umo unachitira nsembe yaufa cha m'mawa ndi nsembe yake yothira, akhale fungo lokoma, nsembe yamoto ya Yehova. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201441 Ndi mwanawankhosa wina ukonze madzulo; umkonze umo unachitira nsembe yaufa cha m'mawa ndi nsembe yake yothira, akhale fungo lokoma, nsembe yamoto ya Yehova. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa41 Tsono uzipereka mwanawankhosa wachiŵiriyo madzulo ndithu. Pamodzi ndi mwanawankhosayo, uziperekanso chopereka chachakudya ndi cha chakumwa, monga zam'maŵa zija, kuti zipereke fungo lokoma ndipo zikhale nsembe yopsereza yopereka kwa Chauta. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero41 Upereke mwana wankhosa winayo madzulo pamodzi ndi chopereka chachakudya monga poyamba paja ndi chopereka chachakumwa monga mmawa kuti ikhale fungo lokoma la chopereka chachakudya kwa Yehova. Onani mutuwo |
Ndipo mfumu Ahazi analamulira Uriya wansembe, kuti, Paguwa la nsembe lalikulu uzifukiza nsembe yopsereza yam'mawa, ndi nsembe yaufa yamadzulo, ndi nsembe yopsereza ya mfumu, ndi nsembe yake yaufa, pamodzi ndi nsembe yopsereza ya anthu onse a m'dziko, ndi nsembe yao yaufa, ndi nsembe zao zothira; uziwaza pa ilo mwazi wonse wa nsembe yopsereza, ndi mwazi wonse wa nsembe yophera; koma guwa la nsembe lamkuwa ndi langa, lofunsira nalo.